Yesu Anacitila Umboni Coonadi
Yesu anacitila umboni coonadi cokhudza colinga ca Mulungu
-
M’MAWU: Mokangalika iye anali kulalikila coonadi conena za Ufumu wa Mulungu
-
M’ZOCITA: Umoyo wake unaonetsa poyela kuti maulosi a Mulungu amakwanilitsika
Pokhala ophunzila a Yesu, na ise timacitila umboni coonadi
-
M’MAWU: Ngakhale ena atinyoze, mokangalika timalalikila uthenga wabwino wonena za kukhazikitsidwa kwa Ufumu wa Mulungu, umene Khristu ndiye Mfumu yake
-
M’ZOCITA: Timaonetsa kuti tikucilikiza ufumu wa Yesu mwa kuyesetsa kukhala na makhalidwe aumulungu komanso mwa kupewa kutengako mbali m’zandale