October 30–November 5
YOWELI 1-3
Nyimbo 143 na Pemphelo
Mau Oyamba (3 mineti kapena kucepelapo)
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
“Ana Anu Aamuna ndi Ana Anu Aakazi Adzanenela”: (10 min.)
[Tambitsani vidiyo yakuti: Mfundo Zokhudza Buku la Yoweli.]
Yow. 2:28, 29—Akhristu odzozedwa amatumikila monga olankhulilako Yehova (w02 8/1 peji 15 mapa. 4-5; jd peji 167 pala. 4
Yow. 2:30-32—Oitanila pa dzina la Yehova okha ni amene adzapulumuka tsiku loyofya la Yehova (w07 10/1 peji 13 pala. 2)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (8 min.)
Yow. 2:12, 13—Kodi mavesi aya atiphunzitsa ciani za kulapa kweni-kweni? (w07 10/1 peji 13 pala. 5)
Yow. 3:14—Kodi ‘cigwa coweluzila mlandu’ n’ciani? (w07 10/1 peji 13 pala. 3)
Kodi imwe pacanu, kuŵelenga Baibo kwa wiki ino kwakuphunzitsani ciani za Yehova?
Ni cuma ca kuuzimu cina citi cimene mwapeza pa kuŵelenga Baibo kwa wiki ino?
Kuŵelenga Baibo: (4 mineti kapena kucepelapo) Yow. 2:28–3:8
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Ulendo Woyamba: (2 mineti kapena kucepelapo) Kakhadi kongenela pa JW.ORG
Ulendo Wobwelelako: (4 mineti kapena kucepelapo) Kakhadi kongenela pa JW.ORG—Kakhadi kanagaŵilidwa kale paulendo woyamba. Pitilizani makambilano ndipo tsilizani mwa kuyelekeza monga mufuna kum’tambitsa vidiyo ya pa jw.org.
Phunzilo la Baibo: (6 mineti kapena kucepelapo) lv peji 196-197 mapa. 3-5
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Yehova Amatithandiza Kupilila Mayeselo: (9 min.) Tambitsani vidiyo yakuti Yehova Ndiye Nsanja Yanga Yolimba. Ndiyeno afunseni mafunso aya omvetsela. Ni mayeselo ati amene banja la m’bale Henschel linakumana nawo? Kodi cikhulupililo ca makolo cimalimbikitsa bwanji ana awo? Nanga Yehova angakulimbitseni bwanji monga anacitila kwa m’Bale Henschel?
Khala Bwenzi la Yehova—Dzina la Yehova: (6 min.) Tambitsani vidiyo yakuti Khala Bwenzi la Yehova—Dzina la Yehova. Ndiyeno pemphani ana angapo kubwela ku pulatifomu na kuwafunsa kuti: Kodi dzina la Yehova limatanthauzanji? Kodi Yehova analenga zinthu zabwanji? Nanga angakuthandizeni bwanji?
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (30 min.) kr nkhani 20 peji 17-19 na mabokosi “Nchito Imene Inasintha Moyo Wake” na “Anchito Odzipeleka Padziko Lonse Amathandiza Kwambili”; komanso kabokosi kobwelelamo “Kodi Mumaona Kuti Ufumu wa Mulungu ndi Weniweni?”
Kubwelelamo na Kuchulako za Wiki Yotsatila (3 min.)
Nyimbo 72 na pemphelo