Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Khalani Woŵelenga Malemba Wakhama

Khalani Woŵelenga Malemba Wakhama

Kodi mungakonde kukhala wokhulupilika pa mayeselo monga Danieli? Danieli anali kuŵelenga Mau a Mulungu mwakhama, kuphatikizapo maulosi ozama. (Dan. 9:2) Kuŵelenga Baibo mwakhama kungakuthandizeni kukhalabe wokhulupilika. Motani? Kungalimbitse cikhulupililo canu cakuti malonjezo a Yehova adzakwanilitsika. (Yos. 23:14) Kungakuthandizeninso kuonjezela cikondi canu pa Mulungu, na kuti muzicita zinthu zabwino. (Sal. 97:10) Koma kodi mungayambile pati? Onani malingalilo otsatilawa.

  • Kodi niziphunzila ciani? Cizoloŵezi cabwino ca kuŵelenga cimaphatikizapo kukonzekela misonkhano ya mpingo. Kuŵelenga Baibo kwa wiki na wiki kungakupindulitseni ngako ngati mupatula nthawi yofufuza mfundo zimene simunazimvetsetse. Kuonjezela apo, ena amakonda kuŵelenganso maulosi a m’Baibo, mbali zosiyana-siyana za cipatso ca mzimu wa Mulungu, maulendo aumishonale a mtumwi Paulo, ngakhalenso za cilengedwe ca Yehova. Ngati mwaganiza funso linalake, ilembeni kuti mukaifufuze pa nthawi yoŵelenga Baibo.

  • Ni kuti kumene ningafufuze? Tambani vidiyo yakuti Zida Zofufuzila Cuma ca Kuuzimu kuti muone zida zimene zingakuthandizeni. Mwacitsanzo, yesani kufufuza maulamulilo amphamvu a padziko oimilidwa na zilombo zochulidwa pa Danieli 7.

  • Kodi nifunika kumaŵelenga kwa nthawi yaitali bwanji? Cofunika kwambili ni kuŵelenga nthawi zonse kuti mukhale wathanzi mwauzimu. Ponena za nthawi, mungayambe pang’ono-pang’ono na kuonjezela m’kupita kwa nthawi. Kuphunzila Mau a Mulungu kuli monga kufufuza cuma cobisika. Mukamapeza cuma cina, mumapitiliza kufufuza. (Miy. 2:3-6) Cikhumbo canu cophunzila Mau a Mulungu cidzaonjezeka, ndipo kuphunzila Baibo kudzakhala cizoloŵezi canu.—1 Pet. 2:2

KODI ZILOMBO ZA MU DANIELI CAPUTA 7 ZIMAIMILA CIANI?

  • Dan. 7:4

  • Dan. 7:5

  • Dan. 7:6

  • Dan. 7:7

FUNSO LOONJEZELA:

Kodi lemba la Danieli 7:8, 24 linakwanilitsika bwanji?

TSOPANO KAFUFUZENI IZI:

Kodi zilombo za pa Chivumbulutso caputa 13 ziimila ciani?