CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
Cuma Sicimapangitsa Munthu Kukhala Wolungama
Zofari anakamba kuti Mulungu amalanda cuma ca anthu oipa. Pokamba mawuwa, iye anali kutanthauza kuti Yobu ayenela kuti anacimwa (Yobu 20:5, 10, 15)
Yobu anamuyankha kuti: ‘Nanga n’cifukwa ciyani anthu oipa amalemela?’ (Yobu 21:7-9)
Citsanzo ca Yesu cionetsa kuti ngakhale munthu wolungama akhoza kukhala wopanda cuma (Luka 9:58)
ZOYENELA KUZISINKHASINKHA: Kodi cofunika kwambili kwa munthu wolungama n’ciyani, mosasamala kanthu kuti ni wolemela kapena wosauka?—Luka 12:21; w07 8/1 29 ¶12.