UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Zimene Zingakuthandizeni Kupewa Kuzengeleza
Munthu wozengeleza amakankhila kutsogolo zinthu zimene ayenela kucita nthawi yomweyo. Yehu sanazengeleze kugwila nchito imene Yehova anamupatsa, yowononga onse a m’nyumba ya Ahabu. (2 Maf. 9:6, 7, 16) Anthu ena amakamba kuti: “Mwina nidzabatizika m’zaka zingapo zikubwelazi.” Kapena “Posacedwapa nidzayamba kuŵelenga Baibo tsiku lililonse.” Kapenanso kuti “Nidzafunsila upainiya nikadzapeza nchito yabwino.” Malemba angatithandize kupewa kuzengeleza pa zocita zathu zokhudza kulambila.
Kodi malemba otsatilawa angatilimbikitse bwanji kupewa kuzengeleza?
-
Mlal. 5:4
-
Mlal. 11:4
-
1 Akor. 7:29-31
-
Yak. 4:13, 14