UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Kondwelani Pamene Mukuzunzidwa
Akhristu amadziŵa kuti adzazunzidwa. (Yoh. 15:20) Ngakhale kuti cizunzo cimabweletsa nkhawa komanso cimakhala cowawa, timakhala acimwemwe tikapilila.—Mat. 5:10-12; 1 Pet. 2:19, 20.
ONELELANI VIDIYO YAKUTI TINGAKHALEBE OKONDWELA NGAKHALE PA MAZUNZO, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATILAWA:
Kodi mwaphunzila ciyani kwa M’bale Bazhenov pa nkhani ya
-
kufunika koŵelenga Baibo tsiku lililonse?
-
kulandila thandizo locokela kwa Akhristu anzanu? *
-
kupemphela nthawi zonse?
-
kuimba nyimbo za Ufumu?
-
kuuzako ena za cikhulupililo canu?
^ Tingapemphelele abale amene ali m’ndende, ngakhale kuchula maina awo. Komabe, n’zosatheka kuti ofesi ya nthambi ilembele kalata aliyense wa iwo.