UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Muziyembekezela Mapeto a Dzikoli Mopanda Mantha
Yehova wakhala akulilezela mtima dziko loipali. Koma posacedwapa, kuleza mtima kumeneko kudzatha. Zipembedzo zonyenga zidzawonongedwa, ndipo mgwilizano wa mitundu udzaukila anthu a Mulungu. Kenako, Yehova adzawononga anthu oipa pa Aramagedo. Akhristu amayembekezela mwacidwi zocitika zofunika komanso zocititsa cidwi zimenezi.
Komabe, sitidziŵa zonse zokhudza cisautso cacikulu. Mwacitsanzo, sitidziŵa nthawi yeniyeni imene cidzayamba. Sitidziŵa kuti olamulila andale adzapeleka zifukwa zotani poukila zipembedzo. Sitidziŵanso kuti mgwilizano wa mitundu udzaukila anthu a Mulungu kwa nthawi yaitali bwanji, komanso kuti kuukilako kudzaloŵetsamo ciyani. Cina, sitikudziŵa njila yeni-yeni imene Yehova adzagwilitsa nchito powononga anthu oipa pa Aramagedo.
Komabe, Malemba amatiuza zonse zofunikila n’colinga cakuti tiziyembekezela zakutsogolo mwacidalilo komanso molimba mtima. Mwacitsanzo, tidziŵa kuti tili kumapeto kwa ‘masiku otsiliza.’ (2 Tim. 3:1) Tidziŵanso kuti kuukila kwa zipembedzo zonyenga ‘kudzafupikitsidwa’ n’colinga cakuti cipembedzo coona cisakawonongedwe. (Mat. 24:22) Tidziŵanso kuti Yehova adzapulumutsa anthu ake. (2 Pet. 2:9) Cina, tidziŵa kuti uyo amene Yehova anamusankha kuti akawononge anthu oipa na kuteteza a khamu lalikulu pa Aramagedo ni wolungama komanso ni wamphamvu.—Chiv. 19:11, 15, 16.
Mosakayikila, zocitika zam’tsogolomu zidzapangitsa anthu “kukomoka cifukwa ca mantha.” Komabe, tikamaŵelenga na kusinkhasinkha mmene Yehova anapulumutsila atumiki ake kumbuyoku, komanso zimene waulula ponena za kutsogolo, tidzatha “kuimilila na kutukula mitu” yathu mwacidalilo podziŵa kuti cipulumutso cathu cayandikila.—Luka 21:26, 28.