November 15-21
YOSWA 23-24
Nyimbo 50 na Pemphelo
Mawu Oyamba (Mph. 1)
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Malangizo Othela a Yoswa kwa Aisiraeli”: (Mph. 10)
Kufufuza Cuma Cauzimu: (Mph. 10)
Yos. 24:2—Kodi Tera, amene anali tate wake wa Abulahamu anali kulambila mafano? (w04 12/1 11 ¶10)
Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, ni mfundo yopindulitsa iti imene munapeza yokhudza Yehova, ulaliki, kapena mfundo ina iliyonse?
Kuŵelenga Baibo: (Mph. 4) Yos. 24:19-33 (th phunzilo 11)
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Ulendo Woyamba: (Mph. 3) Mukayamba na makambilano acitsanzo, mwininyumba akambe mawu ofala kwanuko ofuna kukanila ulaliki, koma mwaluso loŵelani pa mawu amenewo. (th phunzilo 2)
Ulendo Wobwelelako: (Mph. 4) Yambani na makambilano acitsanzo. Gaŵilani kabuku kakuti Kondwelani na Moyo Kwamuyaya! (th phunzilo 20)
Phunzilo la Baibo: (Mph. 5) lffi phunzilo 01 cidule cake, mafunso obweleza, na zocita (th phunzilo 3)
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Pewani Mayanjano Oipa Kunchito: (Mph. 7) Kukambilana. Onetsani vidiyo yakuti Muzipewa Zinthu Zimene Zingakulepheletseni Kukhala Okhulupilika—Mayanjano Oipa. Kenako funsani omvetsela mafunso awa: Kodi mayanjano oipa kunchito anam’khudza bwanji mlongo wa mu vidiyoyi? Ni masinthidwe otani amene anapanga? Nanga kucita zimenezo kunam’thandiza bwanji? Kodi mwaphunzilamo ciani mu vidiyo imeneyi pa nkhani ya kupewa mayanjano oipa?
Pezani Mabwenzi M’malo Osayembekezeleka: (Mph. 8) Kukambilana. Onetsani vidiyo yakuti Mabwenzi M’malo Osayembekezeleka. Kenako funsani omvetsela mafunso awa: Ni mavuto otani amene anapangitsa Akil kuyamba kugwilizana na anthu a makhalidwe oipa kusukulu? Kodi anapeza bwanji mabwenzi abwino mumpingo? Kodi mwaphunzila ciani mu vidiyo imeneyi pa nkhani yopeza mabwenzi abwino?
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (Mph. 30) lfb phunzilo 64
Mawu Othela (Mph. 3)
Nyimbo 3 na Pemphelo