November 19-25
MACHITIDWE 4-5
Nyimbo 73 na Pemphelo
Mawu Oyamba (3 min. olo kucepelapo)
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Anapitiliza kulankhula Mawu a Mulungu Molimba Mtima”: (10 min.)
Mac. 4:5-13—Olo kuti Petulo na Yohane anali “osaphunzila ndiponso anthu wamba,” iwo sanaleke kuteteza cikhulupililo cawo kwa olamulila, na alembi (w08 9/1 peji 15, bokosi; w08 5/15 peji 30 pala. 6)
Mac. 4:18-20—Ngakhale kuti Petulo na Yohane anaopsezedwa, iwo sanaleke kulalikila
Mac. 4:23-31—Akhristu a m’nthawi ya atumwi anadalila mzimu woyela wa Yehova kuti akhale olimba mtima (it-1 peji 128 pala. 3)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (8 min.)
Mac. 4:11—Kodi Yesu ni “mwala wofunika kwambili wapakona” m’lingalilo lanji? (it-1 peji 514 pala. 4)
Mac. 5:1—N’cifukwa ciani Hananiya na Safira anagulitsa munda wawo? (w13 3/15 peji 15 pala. 4)
Kodi imwe pacanu, kuŵelenga Baibo kwa wiki ino kwakuphunzitsani ciani za Yehova?
Ni cuma ca kuuzimu cina citi cimene mwapeza pa kuŵelenga Baibo kwa wiki ino?
Kuŵelenga Baibo: (4 min. olo kucepelapo) Mac. 5:27-42
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Ulendo Woyamba: (2 min. olo kucepelapo) Yambani na makambilano acitsanzo. Mwininyumba akambe zimene anthu a m’gawo lanu amakamba posafuna kuwalalikila.
Kubwelelako Koyamba: (3 min. olo kucepelapo) Yambani na makambilano acitsanzo. Mwininyumba akukuuzani kuti si Mkhristu.
Vidiyo ya Kubwelelako Kaciŵili: (5 min.) Tambitsani na kukambilana vidiyoyi.
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Nyimbo 82 na Pemphelo
“Mapindu a pa Dziko Lonse a Ulaliki wa pa Kasitandi”: (15 min.) Nkhani yokambilana yokambiwa na woyang’anila utumiki. Tambitsani vidiyoyi. Ngati mpingo wanu umaseŵenzetsa thebulo kapena kasitandi pocita ulaliki wapoyela, onetsani zimenezo kwa omvela. Fotokozani makonzedwe a mpingo wanu. Ngati nthawi ilipo, fotokozani cocitika cabwino kapena citani citsanzo ca zimene zinacitikazo. Fotokozani zimene ofalitsa angacite kuti azicitako ulaliki umenewu.
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 43 pala. 8-18
Kubwelelamo na Kuchulako za Wiki Yotsatila (3 min.)
Nyimbo 64 na Pemphelo