UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Khalanibe Achelu ndi Okangalika Zinthu Zikasintha mu Umoyo Wanu
Kusintha n’kosapeweka, maka-maka m’nthawi ino ya masiku otsiliza. (1 Akor. 7:31) Kaya kusinthako tinali kukuyembekezela kapena ayi, kwabwino kapena koipa, kukhoza kusokoneza kulambila kwathu, ndi ubwenzi wathu na Yehova. Nanga n’ciani cingatithandize kukhalabe achelu ndi okangalika pa nthawi ya masinthidwe? Tambani vidiyo yakuti Kukhalabe Olimba Mwauzimu Pamene Mwasamuka, ndiyeno yankhani mafunso aya:
-
Ni malangizo ati amene m’bale wina anapeleka kwa tate uja?
-
Kodi mfundo ya pa Mateyu 7:25 inagwila nchito bwanji pa banja lija?
-
Kodi banja lija linakonzekela bwanji za kusamuka kwawo? Nanga zimenezi zinawathandiza bwanji?
-
N’ciani cinathandiza banja lija kujaila mu mpingo watsopano na gawo lake?
Kusintha kwakukulu kumene kwanikhudza posacedwa:
Ningaseŵenzetse bwanji mfundo za m’vidiyo imeneyi pa umoyo wanga?