Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | MIKA 1-7

Kodi Yehova Amafunanji kwa Ise?

Kodi Yehova Amafunanji kwa Ise?

6:6-8

Yehova amadziŵa zofooka zathu, ndipo satipempha kucita zimene sitingakwanitse. Kwa Mulungu, unansi wathu ndi abale athu ni wofunika kwambili pa kulambila kwa zoona. Ngati tifuna kuti Yehova alandile nsembe zathu, tifunika kukonda na kulemekeza abale athu.