May 5-11
MIYAMBO 12
Nyimbo 101 ndi Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)
1. Kugwila Nchito Mwakhama Kumapindulitsa
(Mph. 10)
Musamataye nthawi kufunafuna zinthu zopanda pake (Miy. 12:11)
Muzigwila nchito mwakhama (Miy. 12:24; w16.06 30 ¶5)
Mudzafupidwa cifukwa cogwila nchito mwakhama (Miy. 12:14)
ZIMENE MUNGACITE: Kugwila nchito mwakhama kumakhala kosangalatsa mukamaganizila mmene kumapindulitsila ena.—Mac. 20:35; w15 2/1 5 ¶4-6.
2. Kufufuza Cuma Cauzimu
(Mph. 10)
-
Miy. 12:16—Kodi mfundo ya palembali ingathandize bwanji munthu akamakumana ndi mavuto? (ijwyp-CN nkhani 95 ¶10-11)
-
Pa kuwelenga Baibulo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutifotokozelako?
3. Kuwelenga Baibulo
(Mph. 4) Miy. 12:1-20 (th phunzilo 5)
4. Kuyambitsa Makambilano
(Mph. 2) KUNYUMBA NDI NYUMBA. (lmd phunzilo 1 mfundo 4)
5. Kuyambitsa Makambilano
(Mph. 3) KUNYUMBA NDI NYUMBA. M’pempheni kuti muziphunzila naye Baibulo. (lmd phunzilo 5 mfundo 4)
6. Kubwelelako
(Mph. 3) ULALIKI WAMWAYI. Onetsani webusaiti yathu kwa munthu amene ali ndi ana. (lmd phunzilo 9 mfundo 3)
7. Kufotokoza Zimene Mumakhulupilila
(Mph. 3) Citsanzo. ijwfq nkhani 3—Mutu: Kodi Mumakhulupilila Kuti Cipembedzo Canu Cokha Ndiye Coona? (lmd phunzilo 4 mfundo 3)
Nyimbo 21
8. Yehova Angatithandize Tikamakumana Ndi Mavuto Azacuma
(Mph. 15) Kukambilana.
Kodi mumada nkhawa cifukwa cosowa nchito, kapena poganiza kuti nchito yanu ingathe? Kapenanso mumaona kuti simupeza ndalama zokwanila zokuthandizani pali pano kapena mukadzakalamba? Mavuto azacuma m’dzikoli amabwela mosayembekezeleka. Komabe, Yehova amatitsimikizila kuti ngati taika cifunilo cake patsogolo, nthawi zonse iye adzatipatsa zimene timafunikila. Adzacita zimenezi ngakhale titakumana ndi mavuto azacuma mosayembekezela.—Sal. 46:1-3; 127:2; Mat. 6:31-33.
Tambitsani VIDIYO yakuti Yehova Sanatigwilitsepo Mwala. Kenako funsani omvela kuti:
-
Kodi mwaphunzilapo ciyani pa zimene zinacitikila m’bale Alvarado?
Welengani 1 Timoteyo 5:8. Kenako funsani omvela kuti:
-
Kodi lembali lalimbitsa bwanji cikhulupililo canu cakuti Yehova sadzalephela kupatsa alambili ake zimene amafunikila?
Onani mfundo zingapo za m’Baibulo zimene zingakuthandizeni mukakumana ndi mavuto azacuma:
-
Muzikhala umoyo wosalila zambili, ndipo muzipewa nkhongole zosafunikila komanso kugula zinthu zosafunikila. —Mat. 6:22
-
Sankhani nchito komanso maphunzilo amene angakupatseni mpata kuti muziika zinthu zauzimu patsogolo.—Afil. 1:9-11
-
Muzikhala odzicepetsa komanso okonzeka kusintha. Ngati mungacotsedwe nchito, muzikhala okonzeka kugwila nchito iliyonse imene ingakuthandizeni kupeza zofunikila za banja lanu, ngakhale yooneka yotsika.—Miy. 14:23
-
Muzikhala okonzeka kugawilako ena zomwe muli nazo, ngakhale ngati inunso muli ndi zocepa.—Aheb. 13:16
9. Phunzilo la Baibulo la Mpingo
(Mph. 30) bt mutu 26 ¶1-8, mabokosi pa masamba 204, 208