UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Kodi Mumaigwilitsa Nchito Mofikapo Baibo Yongomvetsela?
Kodi Baibo yongomvetsela ni yotani? Baibo yongomvetsela ni Baibo ya Dziko Latsopano yokonzedwanso imene mawu ake anajambulidwa. Ikutulutsidwa pang’ono-pang’ono m’zinenelo zambili. Cimodzi cocititsa cidwi na Baiboyi n’cakuti mawu a munthu aliyense m’Baibo anaŵelengedwa na munthu wosiyana. Mawu ake anaŵelengedwa motsindika komanso na mzimu wake pofuna kumveketsa molondola uthenga wa m’Baibo.
Kodi ena apindula bwanji na Baibo yongomvetsela? Anthu ambili amene amakonda kumvetsela Baibo imeneyi aona kuti imawathandiza kumvetsa Mawu a Mulungu mosavuta. Iwo aona kuti kumvetsela mawu a anthu a m’Baibo akuŵelengedwa na anthu osiyana-siyana, kumawathandiza kuona m’maganizo mwawo zocitika za m’Baibo na kumvetsetsa zimene zinalembedwazo. (Miy. 4:5) Enanso ambili amaona kuti kumvetsela Baibo imeneyi kumawatsitsimula akakhala na nkhawa.—Sal. 94:19.
Kumvetsela Mawu a Mulungu akuŵelengedwa mokweza kungasinthe kwambili umoyo wathu. (2 Mbiri 34:19-21) Ngati Baibo yongomvetsela, kaya mbali yake kapena yathunthu, ipezeka m’cinenelo cimene mumamva, bwanji osakonza zakuti muziimvetsela nthawi zonse pa pulogilamu yanu yauzimu?
ONELELANI VIDIYO YAKUTI NCHITO YOPANGA BAIBO YONGOMVETSELA—MBALI YAKE, KENAKO YANKHANI FUNSO ILI:
N’ciyani cakucititsani cidwi pa nchito yopanga Baibo yongomvetsela?