May 18-24
GENESIS 40-41
Nyimbo 8 na Pemphelo
Mawu Oyamba (1 min.)
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Yehova Anapulumutsa Yosefe”: (10 min.)
Gen. 41:9-13—Farao anamva kuti Yosefe amakwanitsa kumasulila maloto (w15 2/1 14 ¶4-5)
Gen. 41:16, 29-32—Yehova anathandiza Yosefe kumasulila maloto a Farao (w15 2/1 14-15)
Gen. 41:38-40—Yosefe anakhala wolamulila waciŵili kwa Farao mu Iguputo (w15 2/1 15 ¶3)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (10 min.)
Gen. 41:14—N’cifukwa ciani Yosefe anagela tsitsi lake asanapite kukaonekela pamaso pa Farao? (w15 11/1 9 ¶1-3)
Gen. 41:33—Tikaona mmene Yosefe anali kukambila na Farao, zitithandiza kudziŵa ciani? (w09 11/15 28 ¶14)
Pa kuŵelenga Baibo kwa wiki ino, ni mfundo yopindulitsa iti imene munapeza yokhudza Yehova Mulungu, ulaliki, kapena mbali ina iliyonse?
Kuŵelenga Baibo: (4 min. olo kucepelapo) Gen. 40:1-23 (th phunzilo 2)
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Vidiyo ya Ulendo Wobwelelako Woyamba: (5 min.) Kukambilana. Tambitsani vidiyoyi, ndiyeno funsani omvetsela: Kodi n’ciani caonetsa kuti mwamuna na mkazi wake anakonzekela pamodzi ulendo wobwelelako umenewu? Kodi m’bale wacita ciani kuti amveketse bwino cifukwa coŵelengela lemba?
Ulendo Wobwelelako Woyamba: (4 min. olo kucepelapo) Seŵenzetsani makambilano acitsanzo. (th phunzilo 11)
Ulendo Wobwelelako Woyamba: (5 min. olo kucepelapo) Yambani na makambilano acitsanzo. Ndiyeno gaŵilani cofalitsa ca m’Thuboksi Yathu. (th phunzilo 13)
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Khalani Monga Yosefe—Pililanibe Pamene Akukucitilani Zopanda Cilungamo: (6 min.) Yambani mwa kutambitsa vidiyo yakuti, Khala Bwenzi la Yehova—Pililanibe Pamene Akukucitilani Zopanda Cilungamo. Ndiyeno pemphani ana kuti abwele ku pulatifomu, ndipo afunseni mafunso aya: Kodi Kalebe na Sofiya anacitilidwa zinthu zotani zopanda cilungamo? Kodi muona kuti iwo anaphuzila ciani pa zimene Yosefe anakumana nazo?
Zofunikila za Mpingo: (9 min.)
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 115
Mawu Othela (3 min. olo kucepelapo)
Nyimbo 124 na Pemphelo