2 AKORINTO 4-6
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU |“Sitikubwelela M’mbuyo”
4:16-18
Yelekezelani kuti mabanja aŵili akukhala m’nyumba imodzi koma yamakomo aŵili osiyana. Nyumbayo niyakale komanso yowonongeka. Banja loyamba ni lokwinyilila komanso losakondwa kukhala m’nyumbayo, ndipo m’pomveka. Koma banja laciŵili ni lacimwemwe. Cifukwa ciani? Cifukwa posacedwa lidzakukila m’nyumba yatsopano yokongola.
Olo kuti “cilengedwe conse cikubuula limodzi ndi kumva zoŵaŵa mpaka pano,” atumiki a Yehova ali monga banja laciŵili lija. Ali na ciyembekezo cimene cimaŵapatsa cimwemwe. (Aroma 8:22) Pali pano tili na mavuto amene tikukumana nawo. Palinso mavuto amene takhala tikukumana nawo kwa zaka zambili. Mavuto onsewa ni “akanthawi ndipo ndi opepuka” tikawayelekezela na moyo wosatha umene Mulungu adzatipatsa m’dziko latsopano. Kusumika maganizo athu pa madalitso a kutsogolo mu Ufumu wa Mulungu, kudzatipatsa cimwemwe, ndipo sitidzataya mtima.