March 6-12
YEREMIYA 1-4
Nyimbo 23 na Pemphelo
Mau Oyamba (3 mineti kapena kucepelapo)
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
“Ine Ndili ndi Iwe Kuti Ndikulanditse”: (10 min.)
[Tambitsani vidiyo yakuti Mfundo Zokhudza Buku la Yeremiya.]
Yer. 1:6—Yeremiya anazengeleza kulandila udindo watsopano (w11 3/15 peji 29 pala. 4)
Yer. 1:7-10, 17-19—Yehova analonjeza Yeremiya kuti adzam’limbitsa na kum’thandiza (w05 12/15 peji 23 pala. 18; jr peji 88 pala. 14-15)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (8 min.)
Yer. 2:13, 18—Ni zinthu ziŵili ziti zoipa zimene Aisiraeli osakhulupilika anacita? (w07 3/15 peji 9 pala. 8)
Yer. 4:10—Kodi Yehova ‘anapusitsa’ anthu ake m’lingalilo liti? (w07 3/15 peji 9 pala. 4)
Kodi ine pacanga, kuŵelenga Baibo kwa wiki ino kwaniphunzitsa ciani za Yehova?
Ni mfundo ziti pa kuŵelenga Baibo kwa wiki ino zimene ine pacanga ningaseŵenzetse mu ulaliki?
Kuŵelenga Baibo: (4 mineti kapena kucepelapo) Yer. 4: 1-10
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Konzekelani Maulaliki a Mwezi Uno: (15 min.) Kukambilana kozikidwa pa “Maulaliki a Citsanzo.” Tambitsani vidiyo yake iliyonse, ndiyeno kambilanani zimene mwaphunzilapo.
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Zimene Gulu Likukwanilitsa: (7 min.) Tambitsani vidiyo yakuti Zimene Gulu Likukwanilitsa ya March.
Kampeni Yoitanila Anthu ku Cikumbutso Idzayamba pa 18 March: (8 min.) Nkhani yokambidwa na woyang’anila nchito yocokela mu Kabuku ka Umoyo na Utumiki, ka February 2016 peji 8. Patsani onse m’gulu kapepa ka ciitano ca Cikumbutso ndi kukambilana. Fotokozani pulogilamu imene yakonzedwa yofolela gawo lanu.
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (30 min.) kr nkhani 9 mapa. 10-15, chati pa peji 90, na bokosi pa peji 93, 96-97
Kubwelelamo na Kuchulako za Wiki Yotsatila (3 min.)
Nyimbo 74 na Pemphelo