EKSODO 4-5
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU |“Ine Ndidzakhala Nawe Polankhula”
4:10-15
Ndi thandizo la Yehova, Mose anagonjetsa mantha ake. Kodi tingaphunzilepo ciani pa zimene Yehova anauza Mose?
-
Tizipewa kusumika maganizo athu pa zinthu zimene timalephela kucita
-
Tiyenela kukhala na cidalilo cakuti Yehova adzatipatsa zonse zofunikila kuti tikwanilitse nchito imene tapatsidwa
-
Cikhulupililo cathu mwa Mulungu cidzatithandiza kuti tisamaope anthu
Kodi Yehova wanithandiza bwanji kupitiliza kulalikila ngakhale panthawi zovuta?