UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Kodi Yehova Aiona Bwanji Nkhaniyi?
Tikafuna kupanga zosankha, zazikulu kapena zazing’ono, tizidzifunsa kuti, ‘Kodi Yehova aiona bwanji nkhaniyi?’ Ngakhale kuti sitingadziŵe maganizo onse a Yehova, iye kupitilila m’Mawu ake, amatiuza zambili zimene zingatithandize kukhala “wokonzeka mokwanila kucita nchito iliyonse yabwino.” (2 Tim. 3:16, 17; Aroma 11:33, 34) Yesu anazindikila cifunilo ca Yehova, ndipo anaciika patsogolo mu umoyo wake. (Yoh. 4:34) Mofanana na Yesu, tiyeni ticite zimene tingathe kuti tizipanga zosankha zokondweletsa Yehova.—Yoh. 8:28, 29; Aef. 5:15-17.
TAMBITSANI VIDIYO YAKUTI PITILIZANI KUZINDIKILA CIFUNILO CA YEHOVA (LE 19:18), NDIYENO YANKHANI MAFUNSO AYA:
-
N’cifukwa ciani tifunika kuseŵenzetsa mfundo za m’Baibo mu umoyo wathu?
-
Ni mfundo ziti za m’Baibo zimene zingatithandize kusankha nyimbo zoyenela?
-
Ni mfundo ziti za m’Baibo zimene zingatithandize pa mavalidwe na kudzikonza?
-
Ni mbali zina ziti mu umoyo wathu zimene zingafune kuti tiseŵenzetse mfundo za m’Baibo?
-
Kodi tingacite ciani kuti tikulitse luso lathu la kuzindikila cifunilo ca Yehova?