Kanizani Ziyeso Mmene Yesu Anacitila
Satana amafuna kuwononga ubwenzi wathu na Yehova mwa kuticititsa kulaka-laka zoipa. Iye amayesa munthu aliyense kulingana na mmene zinthu zilili mu umoyo wake komanso zimene amakonda.
Ni cida camphamvu citi cimene Yesu anaseŵenzetsa kuti asagonje ku mitundu itatu ya ziyeso zimene anakumana nazo? (Aheb. 4:12; 1 Yoh. 2:15, 16) Ningatengele bwanji citsanzo cake?