August 11-17
MIYAMBO 26
Nyimbo 88 ndi Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)
1. Pewani Kugwilizana ndi “Anthu Opusa”
(Mph. 10)
“Munthu wopusa” sayenela kulemekezedwa (Miy. 26:1; it-2-E 729 ¶6)
“Anthu opusa” nthawi zambili amafunika kupatsidwa cilango camphamvu (Miy. 26:3; w87-CN 10/1 19 ¶12)
“Munthu wopusa” ndi wosadalilika (Miy. 26:6; it-2-E 191 ¶4)
TANTHAUZO: M’Baibo, mawu akuti “munthu wopusa” amakamba za munthu amene amakana kutsatila malangizo ndipo amacita zinthu zosagwilizana ndi mfundo za Mulungu.
2. Kufufuza Cuma Cauzimu
(Mph. 10)
-
Miy. 26:4, 5—N’cifukwa ciyani sitinganene kuti miyambi iwili iyi ikutsutsana? (it-1-E 846)
-
Pa kuwelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutifotokozelako?
3. Kuwelenga Baibo
(Mph. 4) Miy. 26:1-20 (th phunzilo 5)
4. Kuyambitsa Makambilano
(Mph. 3) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Gwilitsani nchito thilakiti poyambitsa makambilano. (lmd phunzilo 1 mfundo 5)
5. Kubwelelako
(Mph. 4) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Pitilizani kukambilana za thilakiti imene munamusiyila pa ulendo wapita. (lmd phunzilo 7 mfundo 4)
6. Kupanga Ophunzila
(Mph. 5) Thandizani wophunzila wanu kukonzekela kuti akalalikile wacibale wake. (lmd phunzilo 11 mfundo 5)
Nyimbo 94
7. Pezani Nzelu Zokuthandizani Kuti Mudzapulumuke mwa Kucita Phunzilo la Munthu Mwini
(Mph. 15) Kukambilana.
Mtumwi Paulo anakumbutsa Timoteyo za kufunika kwa Malemba oyela omwe anawaphunzila kuyambila ali khanda. Cifukwa cophunzila Malembawo, Timoteyo anapeza ‘nzelu zomuthandiza kuti akapulumuke.’ (2 Tim. 3:15) Popeza kuti coonadi ca m’Baibo n’camtengo wapatali, m’pofunika kuti Mkhristu aliyense azipatula nthawi yowelenga Baibo. Nanga bwanji ngati simumakonda kuwelenga?
Welengani 1 Petulo 2:2. Kenako funsani omvela kuti:
-
Kodi n’zotheka kuyamba kukonda kuwelenga Baibo?
-
Kodi tingacite ciyani kuti “tizilakalaka” Mawu a Mulungu?—w18.03 29 ¶6
-
Kodi zida za pa zipangizo zimene gulu lathu lakonza, monga JW Library®, zingatithandize bwanji kuti tizipindula kwambili powelenga Baibo?
Tambitsani VIDIYO yakuti Zimene Gulu Likukwanilitsa—Mfundo Zothandiza Posewenzetsa JW Library. Kenako funsani omvela kuti:
-
Kodi ndi mapindu otani amene mwapeza pogwilitsa nchito JW Library®?
-
Kodi ndi mbali iti yomwe mwapeza kuti ndi yothandiza pa JW Library?
-
Nanga ndi mbali iti yomwe mufuna kuiphunzila ndi kuyamba kuigwilitsa nchito?
8. Phunzilo la Baibo la Mpingo
(Mph. 30) lfb phunzilo 8-9