CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
‘Madalitso Onsewa Adzakupeza’
Anthu amene amamvela mawu a Yehova, amapeza madalitso ambili (Deut. 28:1, 3-6; w10 12/15 19 ¶18)
Madalitso a Yehova amabwela kwa atumiki ake amene amamumvela (Deut. 28:2; w01 9/15 10 ¶2)
Yehova amafuna kuti tizimumvela “mokondwela, ndi mtima wosangalala” (Deut. 28:45-47; w10 9/15 8 ¶4)
Atumiki omvela a Yehova amasangalala na madalitso ambili palipano, ndipo posacedwa adzalandila madalitso oculuka amene iye analonjeza.