EKSODO 10-11
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU |Mose na Aroni aonetsa kulimba kwambili
10:3-6, 24-26, 28; 11:4-8
Mose na Aroni anaonetsa kulimba mtima kwambili pokamba na Farao, amene anali munthu wamphamvu kwambili pa dziko lapansi panthawiyo. N’ciani cinawathandiza kucita zimenezo? Pokamba za Mose, Baibo imati: “Mwa cikhulupililo anacoka mu Iguputo, koma osati cifukwa coopa mfumu ayi, pakuti anapitiliza kupilila moleza mtima ngati kuti akuona Wosaonekayo.” (Aheb. 11:27) Mose na Aroni anali na cikhulupililo colimba mwa Yehova ndipo anamudalila.
Kodi ni mikhalidwe iti imene imafuna kulimba mtima kuti tifotokoze za cikhulupililo cathu kwa munthu wa paudindo?