2 ATESALONIKA 1-3
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2Wosamvela Malamulo Aonekela
2:6-12
Kodi Paulo anali kutanthauza ciani pa mavesiwa?
-
‘Cocititsa’ (vs. 6)—Mwacionekele ni atumwi
-
‘Kuonekela’ (vs. 6)—Atumwi atamwalila, Akhristu a mpatuko anaonekela poyela n’kuyamba kuphunzitsa zinthu zabodza na kucita zinthu mwacinyengo
-
“Cinsinsi ca kusamvela malamulo” (vs. 7)—“Wosamvela malamulo” sanadziŵike bwino-bwino m’nthawi ya Paulo
-
“Wosamvela malamulo” (vs. 8)—Masiku ano ni atsogoleli onse a machalichi acikhristu
-
“Ambuye Yesu adzamuthetsa [wosamvela malamulo]. . . pa nthawi imene kukhalapo kwa Yesuyo kudzaonekele “ (vs. 8)—Yesu adzaonetsa poyela kuti ni Mfumu akadzapeleka ciweluzo ca Yehova pa dongosolo lino la Satana, komanso kwa “wosamvela malamulo”
Kodi mavesiwa akulimbikitsani bwanji pa nkhani ya kulalikila mwakhama ndiponso mwacangu?