July 31–August 6
EZEKIELI 24-27
Nyimbo 81 na Pemphelo
Mau Oyamba (3 mineti kapena kucepelapo)
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
“Ulosi wa Kuwonongedwa kwa Mzinda wa Turo Umalimbitsa Cidalilo m’Mau a Yehova”: (10 min.)
Ezek. 26:3, 4—Kukali zaka 250, Yehova analosela kuti mzinda wa Turo udzaonongewa (si peji 133 pala. 4)
Ezek 26:7-11—Ezekieli anachula mtundu woyamba kudzaukila Turo ndi mtsogoleli wawo (ce peji 216 pala. 3)
Ezek. 26:4, 12—Ezekieli analosela kuti mpanda, manyumba, na dothi la mzinda wa Turo zidzaponyedwa m’madzi (it-1 peji 70)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (8 min.)
Ezek. 24:6, 12—Kodi dzimbili, kapena kuti nguwe, la mphika liimila ciani? (w07 7/1 peji 14 pala. 2)
Ezek. 24:16, 17—N’cifukwa ciani Ezekieli sanaonetse cisoni pamene mkazi wake anamwalila? (w88 9/15 peji 21 pala. 24)
Kodi imwe pacanu, kuŵelenga Baibo kwa wiki ino kwakuphunzitsani ciani za Yehova?
Ni cuma ca kuuzimu cina citi cimene mwapeza pa kuŵelenga Baibo kwa wiki ino?
Kuŵelenga Baibo: (4 mineti kapena kucepelapo) Ezek. 25:1-11
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Ulendo Woyamba: (2 mineti kapena kucepelapo) Kapepa kautheka kalikonse—Yalani maziko a ulendo wobwelelako.
Ulendo Wobwelelako: (4 mineti kapena kucepelapo) Kapepa kauthenga kalikonse—Chulani na kukambilana vidiyo yakuti Kodi Phunzilo la Baibulo Limacitika Bwanji? Koma musaitambitse vidiyoyi.
Phunzilo la Baibo: (6 mineti kapena kucepelapo) bhs peji 23 mapa. 13-15—Itanilani mwininyumba ku misonkhano.
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Kukhulupilila Mau a Mulungu Kumatithandiza Kupilila Mayeselo: (15 min.) Kukambilana kozikidwa pa malemba aya: Yesaya 33:24; 65:21, 22; Yohane 5:28, 29 na Chivumbulutso 21:4. Tambitsani vidiyo yakuti Yamikilani Madalitso a Ufumu (yendani ku mavidiyo BAIBULO). Limbikitsani onse kuti aziyelekezela kuti ali m’dziko latsopano, maka-maka akafooka na mayeselo.
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (30 min.) kr nkhani 15 mapa. 29-36, bokosi lobwelelamo 167
Kubwelelamo na Kuchulako za Wiki Yotsatila (3 min.)
Nyimbo 88 na Pemphelo