Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

CUMA COCOKELA M’MAU A MULUNGU | YESAYA 34-37

Hezekiya anafupidwa cifukwa ca cikhulupililo cake

Hezekiya anafupidwa cifukwa ca cikhulupililo cake

Mfumu Senakeribu ya Asuri inatuma Rabisake ku Yerusalemu kukauza Hezekiya kuti angopeleka mzindawo. Asuri anaseŵenzetsa njila zosiya-nasiyana pofuna kuwayofya Ayuda kuti adzipeleke popanda kumenyana nawo.

  • Kuwapatula. Aiguputo sangakuthandizeni konse.—Yes. 36:6

  • Kuwakaikitsa. Yehova sadzakumenyelani nkhondo cifukwa munam’khumudwitsa.—Yes. 36:7, 10

  • Kuwayofya. Mwacepa kutali-tali kwa asilikali amphamvu a Asuri.—Yes. 36:8, 9

  • Kuwanyengelela. Mukadzipeleka kwa Asuri zinthu zidzakuyendelani bwino.—Yes 36:16, 17

Hezekiya anaonetsa cikhulupililo cosagwedela mwa Yehova

37:1, 2, 14-20, 36

  • Anacita zonse zotheka kuti ateteze mzinda kwa adani odzauzinga

  • Anapemphela kwa Yehova kuti awalanditse, ndi kulimbikitsanso anthu ake kucita cimodzi-modzi

  • Yehova anamufupa mwa kutumiza mngelo amene anapha asilikali acisuri 185,000 usiku umodzi cabe