Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Kodi Mungaphunzile Ciani mu Nyimbo Zopekedwa Koyamba?

Kodi Mungaphunzile Ciani mu Nyimbo Zopekedwa Koyamba?

Kodi mumakonda nyimbo ziti zopekedwa koyamba? Cifukwa? Kodi mumaona kuti zosonyezedwa m’mavidiyo ake n’zothandizadi pa umoyo wa tsiku na tsiku? Pa nkhani zosiyana-siyana za m’nyimbozo, ndiponso maimbidwe ake osiyana-siyana, aliyense amapezapo ya pamtima. Koma colinga cake si kungotisangalatsa cabe ayi.

Nyimbo yopekedwa koyamba iliyonse imatiphunzitsa mfundo zofunikila zimene tingaseŵenzetse mu umoyo na utumiki wathu wacikhristu. Nyimbo zina zimakamba pa kuceleza, mgwilizano, ubwenzi, kulimba mtima, cikondi, komanso cikhulupililo. Zina zimatilimbikitsa kubwelela kwa Yehova, kukhululuka, kusunga umphumphu nthawi zonse, ndiponso kukhala na zolinga zauzimu. Kulinso nyimbo ina yopekedwa koyamba yokamba za kuseŵenzetsa bwino mafoni. Ni mfundo zina ziti zothandiza zimene mwapeza mu nyimbo zopekedwa koyamba?

TAMBITSANI VIDIYO YA NYIMBO YOPEKEDWA KOYAMBA YAKUTI DZIKO LATSOPANO ILI PAFUPI KWAMBILI, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO AYA:

  • Ni madalitso ati akutsogolo amene banja lacikulile likuganizila?—Gen. 12:3

  • Kodi tingalimbitse bwanji cikhulupililo cathu cakuti Yehova angathe kukwanilitsa malonjezo ake?

  • Kodi tidzakondwela kuonananso na ndani m’dziko latsopano limene layandikila?

  • Kodi kuyembekezela Ufumu kumatithandiza bwanji kupilila mavuto amene timakumana nawo?—Aroma 8:25