LEVITIKO 10-11
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU |Cikondi pa Yehova Ciyenela Kukhala Cacikulu Kuposa Cikondi pa Acibale
10:1, 2, 4-7
Kukhulupilika kwathu kwa Yehova kungayesedwe kwambili ngati munthu amene timakonda wacotsedwa mu mpingo. Malangizo amene Yehova anapatsa Aroni ni cenjezo kwa Akhristu amene amayanjana na wacibale wocotsedwa. Cikondi cathu pa Yehova ciyenela kukhala cacikulu kuposa cikondi cathu pa acibale osakhulupilika.
Kodi Akhristu amene amatsatila malangizo a Yehova ponena za ocotsedwa amalandila madalitso otani? —1 Akor. 5:11; 2 Yoh. 10, 11