Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Kodi Mungakonde Kufunsila Kuti Mukaloŵe Sukulu ya Alengezi a Ufumu?

Kodi Mungakonde Kufunsila Kuti Mukaloŵe Sukulu ya Alengezi a Ufumu?

Kodi ndimwe mtumiki wanthawi zonse ndipo muli na zaka zapakati pa 23 na 65? Kodi muli na thanzi labwino ndipo ndimwe wodzipeleka kukatumikila kulikonse kumene kuli alengezi a Ufumu ocepa? Ngati mwayankha kuti inde pa mafunso amenewa, kodi munaganizilapo zofunsila kuti mukaloŵe Sukulu ya Alengezi a Ufumu? Kucokela pamene sukuluyi inayamba, Akhristu a pabanja, abale osakwatila, komanso alongo osakwatiwa ofika m’masauzande afunsilako sukuluyi. Koma tifunabe abale ambili osakwatila kuti afunsile sukuluyi. Pemphani Yehova kuti akulitse cilakolako canu cofuna kum’kondweletsa na kutengela citsanzo ca Mwana wake. (Sal. 40:8; Mat. 20:28; Aheb. 10:7) Kenako ganizilani mmene mungasinthile zinthu pa umoyo wanu kuti mukwanitse kufunsilako sukuluyi.

Kodi Akhristu amene aloŵa sukuluyi amakhala na mwayi wocita mautumiki ati? Ena amawatumiza kuti akatumikile m’magawo a citundu cina kapena kuti akacite ulaliki wapoyela wa m’mizinda ikulu-ikulu. Ndipo ena pambuyo pake amatumikila monga oyang’anila madela ogwilizila, oyang’anila madela, kapena amishonale. Pamene muganizila za utumiki umene mungaciteko m’gulu la Yehova, khalani na maganizo amene Yesaya anali nawo pamene anati: “Ine ndilipo! Nditumizeni!”—Yes. 6:8.

TAMBANI VIDIYO YAKUTI AMISHONALE—ANCHITO OKOLOLA, NDIPO PAMBUYO PAKE YANKHANI MAFUNSO AWA:

  • Kodi amishonale amasankhidwa bwanji?

  • Kodi amishonale amagwila nchito yabwino iti?

  • Ni madalitso ena ati amene utumiki wa umishonale umabweletsa?