TITO 1–FILIMONI
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU |“Kuika Akulu”
Tito 1:5-9
Tito anapatsidwa nchito ‘yoika akulu mu mzinda uliwonse.’ Citsanzo ca m’Baibo ici n’cimene timatsatila masiku ano pamene oyang’anila madela amaika akulu mu mipingo.
BUNGWE LOLAMULILA
Potengela citsanzo ca m’nthawi ya atumwi, Bungwe Lolamulila linapatsa oyang’anila madela mphamvu zoika pa udindo akulu na atumiki othandiza.
OYANG’ANILA MADELA
Woyang’anila dela aliyense afunika kupenda mosamala komanso mwa pemphelo, ziyamikilo zimene akulu apanga zokhudza abale. Akatelo, aike pa udindo amuna amene akuyeneleladi.
AKULU
Pamene akulu aikidwa pa udindo, afunika kukhalabe okwanilitsa ziyenelezo za m’Malemba.