August 7-13
EZEKIELI 28-31
Nyimbo 85 na Pemphelo
Mau Oyamba (3 mineti kapena kucepelapo)
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
“Yehova Anadalitsa Mtundu Wacikunja”: (10 min.)
Ezek. 29:18—Mfumu Nebukadinezara ya ku Babulo sinalandile mphoto iliyonse pambuyo pogonjetsa mzinda wa Turo movutikila (it-2 peji 1136 pala. 4)
Ezek. 29:19—Mfumu Nebukadinezara inapatsidwa dziko la Iguputo monga cofunkha m’malo mwa dziko la Turo (it-1 peji 698 pala. 5)
Ezek. 29:20—Yehova anadalitsa Ababulo cifukwa anacita zimene Iye anali kufuna (g86-E 11/8 peji 27 mapa. 4-5)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (8 min.)
Ezek. 28:12-19—N’cifukwa ciani kacitidwe ka zinthu ka olamulila a ku Turo kalingana ndi ka Satana? (it-2 peji 604 mapa. 4-5)
Ezek. 30:13, 14—Kodi ulosiwu unakwanilitsika bwanji? (w03 7/1 peji 32 mapa. 1-3)
Kodi imwe pacanu, kuŵelenga Baibo kwa wiki ino kwakuphunzitsani ciani za Yehova?
Ni cuma ca kuuzimu cina citi cimene mwapeza pa kuŵelenga Baibo kwa wiki ino?
Kuŵelenga Baibo: (4 mineti kapena kucepelapo) Ezek. 29:1-12
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Konzekelani Maulaliki a Mwezi Uno: (15 min.) Kukambilana kozikidwa pa “Maulaliki a Citsanzo.” Tambitsani vidiyo imodzi imodzi ndipo kambilanani zimene mwaphunzilapo. Limbikitsani ofalitsa kuchulako zocitika za m’delalo polalikila. Komanso, pogaŵila kabuku ka Uthenga Wabwino aziyesetsa kuseŵenzetsa vidiyo yakuti Kodi Mungakonde Kumvelako Uthenga Wabwino?
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Zofunikila za Mpingo: (5 min.) Apo ayi, kambilanani zimene mwaphunzilapo mu Buku Lapachaka la Mboni za Yehova. (yb17 mapeji 35-36 ndi bokosi pa peji 35)
“Kulitsani Makhalidwe Aumulungu—Kudzicepetsa”: (10 min.) Kukambilana. Tambitsani vidiyo yakuti Muzipewa Zinthu Zimene Zingakulepheletseni Kukhala Wokhulupilika—Kudzikuza.
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (30 min.) kr “Cigawo 5—Maphunzilo A Ufumu—Kuphunzitsa Atumiki a Mfumu,” nkhani 16 mapa. 1-5, na mabokosi “Kulambila kwa Pabanja” ndi “Misonkhano ya pa Caka Imene Imagwilizanitsa Anthu a Mulungu”
Kubwelelamo na Kuchulako za Wiki Yotsatila (3 min.)
Nyimbo 20 na Pemphelo