UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Ni Liti Pamene Ningadzacitekonso Upainiya Wothandiza?
Masomphenya a Ezekieli a kacisi aonetsa kuti anthu a Yehova adzapeleka nsembe mofunitsitsa. Kodi inenso ningatengeko mbali motani pa Ni Liti Pamene Ningadzacitekonso Upainiya Wothandiza?—Aheb. 13:15, 16.
Njila imodzi yabwino ngako ni kutengako upainiya wothandiza. Caka ca utumiki ca 2018, cili na miyezi ingapo ili na masiku a Ciŵelu asanu, kapena masiku a Sondo asanu. Izi n’zothandiza maka-maka kwa aja ogwila nchito yolembedwa ndipo nthawi zambili, amapita mu ulaliki pa wikendi. Kuwonjezela apo, ofalitsa angasankhe kukwanilitsa maola 30 kapena 50 m’miyezi ya March na April, ndiponso mwezi umene adzacezeledwa na woyang’anila dela.
Koma bwanji ngati mikhalidwe yanu sikulolani kucitako upainiya wothandiza? Mungatengelepo mwayi wonola luso lanu kapena kuwonjezelako utumiki wanu. Mulimonse mmene zinthu zilili, lekani kuti cikondi cathu pa Yehova citisonkhezele kum’patsa zabwino koposa m’caka ca utumiki ca 2018.—Hos. 14:2.
TAMBANI VIDIYO YAKUTI CIFUKWA CA THANDIZO LA YEHOVA NINGAKWANITSE KUCITA CILICONSE, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO AYA:
-
N’ciani cimasonkhezela Sabina kucita zambili mu utumiki wake kwa Yehova?
-
Kodi citsanzo ca Sabina cakulimbikitsani bwanji?
-
M’caka ca Utumiki ca 2018, ni mwezi kapena miyezi iti imene mungadzaciteko upainiya wothandiza?