Maulaliki a Citsanzo
GALAMUKANI!
Funso: Kodi muganiza kuti munthu angapindule bwanji ngati ayesetsa kuleka zizoloŵezi zoipa?
Lemba: Mlal. 7:8a
Cogaŵila: Nkhani izi zifotokoza mfundo za m’Baibulo zimene zingathandize anthu kusintha zizoloŵezi zawo kuti akhale na umoyo wabwino.
GALAMUKANI!
Funso: Zinthu pa umoyo zimasintha-sintha. Muganiza kuti n’ciani cingatithandize kukhalabe acimwemwe ngati zinthu zina zasintha pa umoyo wathu?
Lemba: Mlal. 7:10
Cogaŵila: [Aonetseni nkhani imene iyambila patsamba 10.] Nkhani iyi ifotokoza mfundo za m’Baibulo zimene zingatithandize ngati zinthu zina zasintha pa umoyo wathu.
MVETSELANI KWA MULUNGU KUTI MUKHALE NDI MOYO WAMUYAYA
Funso: Aliyense wa ife ali na dzina. Ngakhale acibale athu ndi anzathu naonso ali na maina. Nanga Mulungu dzina lake n’ndani?
Lemba: Sal. 83:18
Cogaŵila: Kabuku aka kafotokoza zinthu zina zambili zimene Baibulo imakamba ponena za Mulungu. [Afotokozeleni mwacidule zimene zili pa masamba 6 ndi 7.]
KONZANI ULALIKI WANU
Funso:
Lemba:
Cogaŵila: