Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

UMOYO WATHU WACIKHIRISTU

Kampeni Yapadela Yogaŵila Nsanja ya Mlonda mu September

Kampeni Yapadela Yogaŵila Nsanja ya Mlonda mu September

Anthu padziko lapansi afunika kutonthozedwa. (Mlal. 4:1) M’mwezi wonse wa September, tiyesetse kugaŵila magazini yapadela ya Nsanja ya Mlonda, imene ikamba za citonthozo. Tiyeni tonse tigaŵile magazini imeneyi kwa anthu ambili. Popeza tifuna kukamba ndi anthu mwacindunji n’colinga cakuti tiwalimbikitse, sitiyenela kusiya magaziniyi pa nyumba imene sitinapezepo anthu.

ZIMENE MUNGAKAMBE

“Aliyense amafuna citonthozo nthawi zina. Kodi n’kuti kumene tingacipeze? [Ŵelengani 2 Akorinto 1:3, 4.] Magazini iyi ya Nsanja ya Mlonda ifotokoza mmene Mulungu amatitonthozela.”

Ngati munthu wacita cidwi ndi kulandila magazini, . . .

MUONETSENI VIDIYO YAKUTI N’CIFUKWA CIANI MUYENELA KUPHUNZILA BAIBULO?

Ndiyeno m’pempheni kuti muziphunzila naye Baibulo.

YALANI MAZIKO A ULENDO WOBWELELAKO

Siyani funso limene mudzayankha pa ulendo wobwelelako monga lakuti, “N’cifukwa ciani Mulungu amalolela kuti anthu azivutika?