Uthenga Wabwino Wolembedwa ndi Yohane 8:12-59

  • Atate acitila umboni za Yesu (12-30)

    • Yesu ndi “kuwala kwa dziko” (12)

  • Ana a Abulahamu (31-41)

    • ‘Coonadi cidzakumasulani’ (32)

  • Ana a Mdyelekezi (42-47)

  • Yesu ndi Abulahamu (48-59)

8   12  Kenako Yesu anawauzanso kuti: “Ine ndine kuwala kwa dziko. Aliyense amene amanditsatila sadzayenda mumdima ngakhale pang’ono, koma adzakhala ndi kuwala kwa moyo.” 13  Conco Afarisi anamuuza kuti: “Iwe umadzicitila wekha umboni; koma umboni wako si woona.” 14  Yesu anawauza kuti: “Ngakhale kuti ndimadzicitila ndekha umboni, umboni wanga ndi woona, cifukwa ndidziwa kumene ndinacokela komanso kumene ndikupita. Koma inu simukudziwa kumene ndinacokela ndi kumene ndikupita. 15  Inu mumaweluza potengela maonekedwe akunja,* ine sindiweluza munthu aliyense. 16  Koma ndikati ndiweluze, ciweluzo canga cimakhala colungama, cifukwa sindiweluza ndekha koma ndimaweluzila pamodzi ndi Atate amene anandituma. 17  Komanso m’Cilamulo canu munalembedwa kuti: ‘Umboni wa anthu awili ndi woona.’ 18  Ine ndimadzicitila ndekha umboni, ndipo Atate amene anandituma amandicitilanso umboni.” 19  Ndiyeno iwo anamufunsa kuti: “Atate ako ali kuti?” Yesu anayankha kuti: “Ine simundidziwa ayi, komanso Atate simuwadziwa. Mukanandidziwa ine, mukanadziwanso Atate.” 20  Yesu anakamba mawu amenewa ali m’malo osungila ndalama, pamene anali kuphunzitsa m’kacisi. Koma palibe amene anamugwila cifukwa nthawi yake inali isanakwane. 21  Cotelo iye anawauzanso kuti: “Ine ndikupita, ndipo mudzandifunafuna, koma mudzafa mukali ocimwa. Kumene ine ndikupita simungathe kufikako.” 22  Ndiyeno Ayudawo anayamba kukamba kuti: “Kodi ameneyu akufuna kudzipha? Nanga bwanji akunena kuti, ‘Kumene ine ndikupita simungathe kufikako?’” 23  Iye anapitiliza kuwauza kuti: “Inu ndinu ocokela padziko lapansi, koma ine ndine wocokela kumwamba. Inu ndinu a m’dzikoli, koma ine sindinacokele m’dzikoli. 24  N’cifukwa cake ndakuuzani kuti: Mudzafa mukali ocimwa. Cifukwa ngati simukhulupilila kuti amene munali kumuyembekezela uja ndine, mudzafa mukali ocimwa.” 25  Conco iwo anayamba kumufunsa kuti: “Kodi ndiwe ndani?” Yesu anawayankha kuti: “Nditayilanji nthawi kukamba nanu? 26  Ndili ndi zambili zimene ndingakambe zokhudza inu ndi kupeleka ciweluzo. Kukamba zoona, amene anandituma ndi woona, ndipo zimene ndinamva kwa iye ndimazilankhula m’dzikoli.” 27  Iwo sanazindikile kuti anali kuwauza za Atate. 28  Kenako Yesu anawauza kuti: “Mukadzakweza Mwana wa munthu, mudzadziwa kuti amene munali kuyembekezela uja ndine, komanso kuti sindicita ciliconse congoganiza pandekha. Koma ndimalankhula zinthu zimenezo mogwilizana ndi zimene Atate anandiphunzitsa. 29  Ndipo amene ananditumayo ali nane. Iye sanandisiye ndekha, cifukwa nthawi zonse ndimacita zinthu zomukondweletsa.” 30  Pamene iye anali kukamba zimenezi, anthu ambili anamukhulupilila. 31  Ndiyeno Yesu anapitiliza kuuza Ayuda amene anamukhulupililawo kuti: “Mukapitiliza kusunga mawu anga, ndiye kuti ndinudi ophunzila anga. 32  Mudzadziwa coonadi, ndipo coonadico cidzakumasulani.” 33  Iwo anamuyankha kuti: “Ife ndife ana a Abulahamu, ndipo sitinakhalepo akapolo a munthu aliyense. Ndiye n’cifukwa ciyani ukunena kuti, ‘Mudzamasulidwa’?” 34  Yesu anawayankha kuti: “Ndithudi ndikukuuzani, aliyense amene amacita chimo ndi kapolo wa chimo. 35  Ndiponso kapolo sakhala m’nyumba ya mbuye wake kwamuyaya, koma mwana ndi amene amakhalamo kwamuyaya. 36  Conco ngati Mwana wakumasulani, mudzakhaladi omasuka. 37  Ndidziwa kuti ndinu ana a Abulahamu. Koma mukufuna kundipha cifukwa mawu anga alibe malo mwa inu. 38  Ine ndimakamba zinthu zimene ndinaona pamene ndinali ndi Atate, koma inu mumacita zinthu zimene mwamva kwa atate wanu.” 39  Iwo anamuyankha kuti: “Atate wathu ndi Abulahamu.” Yesu anawauza kuti: “Mukanakhala ana a Abulahamu, mukanacita nchito za Abulahamu. 40  Koma tsopano mufuna kundipha, ine munthu amene ndakuuzani coonadi cimene ndinamva kwa Mulungu. Abulahamu sanacite zimenezi. 41  Inu mukucita nchito za atate wanu.” Iwo anamuuza kuti: “Ife sitinabadwe kucokela mu ciwelewele,* koma tili ndi Atate mmodzi, Mulungu.” 42  Yesu anawauza kuti: “Mulungu akanakhala Atate wanu, mukanandikonda, cifukwa ine ndinabwela kucokela kwa Mulungu ndipo ndili pano. Sindinabwele mwakufuna kwanga, koma Iyeyo ndiye anandituma. 43  N’cifukwa ciyani simukumvetsa zimene ndikukamba? N’cifukwa cakuti simufuna kumvetsela mawu anga. 44  Inu ndinu ocokela kwa atate wanu Mdyelekezi, ndipo mumafuna kucita zokhumba za atate wanuyo. Ameneyo ndi wakupha kucokela paciyambi, ndipo sanapitilize kukhala m’coonadi, cifukwa mwa iye mulibe coonadi. Iye akamakamba bodza amaonetsa mmene alili cifukwa ndi wabodza, komanso ndiye tate wake wa bodza. 45  Koma cifukwa cakuti ndimakuuzani zoona, simundikhulupilila. 46  Ndani wa inu amene ali ndi umboni woonetsa kuti ndacita chimo? Ngati ndimalankhula zoona, n’cifukwa ciyani simundikhulupilila? 47  Wocokela kwa Mulungu amamvetsela mawu a Mulungu. Inu sindinu ocokela kwa Mulungu. Ndiye cifukwa cake simumvetsela.” 48  Ayudawo anamuyankha kuti: “Kodi tikunama ponena kuti, ‘Ndiwe Msamariya ndipo uli ndi ciwanda’?” 49  Yesu anayankha kuti: “Ine ndilibe ciwanda, koma ndimalemekeza Atate, ndipo inu mukundinyoza. 50  Koma ine sindidzifunila ulemelelo ayi, ndi Mulungu amene amafuna kuti ndilemekezedwe, ndipo Iye ndi woweluza. 51  Ndithudi ndikukuuzani, ngati munthu amasunga mawu anga, sadzaona imfa mpang’ono pomwe.” 52  Ayudawo anamuuza kuti: “Tsopano tadziwa kuti ulidi ndi ciwanda. Abulahamu anamwalila, nawonso aneneli anamwalila, koma iwe ukukamba kuti, ‘Ngati munthu amasunga mawu anga sadzaona imfa ngakhale pang’ono.’ 53  Kodi iwe ndiwe wamkulu kuposa Abulahamu atate wathu, amene anamwalila? Aneneli nawonso anamwalila. Ndiye umadziona kuti ndiwe ndani?” 54  Yesu anayankha kuti: “Ndikadzifunila ndekha ulemelelo, ulemelelo wangawo ndi wopanda pake. Atate wanga ndiye amandipatsa ulemelelo, amene inu mumati ndi Mulungu wanu. 55  Mpaka pano inu simumudziwa, koma ine ndimudziwa. Ndipo ngati ndinganene kuti sindimudziwa, ndiye kuti ndingakhale wabodza ngati inu. Koma ndimudziwa ndithu, ndipo ndimasunga mawu ake. 56  Abulahamu atate wanu anakondwela kwambili cifukwa coyembekezela kuona tsiku langa, ndipo ataliona anasangalala.” 57  Kenako Ayudawo anamuuza kuti: “Iwe ukalibe kukwanitsa ngakhale zaka 50, koma ukuti unamuona Abulahamu?” 58  Yesu anawauza kuti: “Ndithudi ndikukuuzani, Abulahamu asanakhaleko n’komwe ine ndinaliko kale.” 59  Conco iwo anatola miyala kuti amuponye nayo, koma Yesu anabisala, kenako anatuluka m’kacisi.

Mawu a m'Munsi

Kapena kuti, “potengela mfundo za anthu.”