Wolembedwa na Mateyo 8:1-34

  • Wakhate acilitsidwa (1-4)

  • Cikhulupililo ca kapitawo wa asilikali (5-13)

  • Yesu acilitsa anthu ambili ku Kaperenao (14-17)

  • Mmene tingatsatilile Yesu (18-22)

  • Yesu aleketsa cimphepo ca mkuntho pa nyanja (23-27)

  • Yesu atumiza ziŵanda m’nkhumba (28-34)

8  Atatsika m’philimo, cikhamu ca anthu cinamutsatila. 2  Ndiyeno kunabwela munthu wakhate, ndipo anamuŵelamila n’kunena kuti: “Ambuye, ngati mufuna munganiyeletse.” 3  Pamenepo Yesu anatambasula dzanja lake n’kumukhudza, ndipo anati: “Nifuna! Khala woyela.” Nthawi yomweyo khate lakelo linatha. 4  Ndiyeno Yesu anamuuza kuti: “Samala kuti usauze aliyense zimenezi. Koma pita ukadzionetse kwa wansembe, ndipo ukapeleke mphatso imene Mose analamula, kuti ukhale umboni kwa iwo.” 5  Ataloŵa mu mzinda wa Kaperenao, kapitawo wa asilikali anabwela kwa iye, n’kuyamba kumucondelela 6  kuti: “Bambo, wanchito wanga ali gone m’nyumba, akudwala matenda ofa ziwalo, ndipo akuzunzika koopsa.” 7  Iye anamuuza kuti: “Nikafika kumeneko, nikam’cilitsa.” 8  Kapitawo uja anamuyankha kuti: “Bambo, ine sindine woyenela kuti inu mukaloŵe m’nyumba mwanga. Koma mungonena mawu, ndipo wanchito wanga acila. 9  Pakuti inenso nili na akulu-akulu amene amanilamulila, ndipo nili na asilikali amene nimawalamulila. Nikauza uyu kuti, ‘Pita!’ amapita, nikauza wina kuti, ‘Bwela!’ amabwela, ndipo nikauza kapolo wanga kuti, ‘Cita ici!’ amacita.” 10  Yesu atamva zimenezi anadabwa kwambili, ndipo anauza amene anali kumutsatila aja kuti: “Kukuuzani zoona, mu Isiraeli sin’napezemo munthu wa cikhulupililo cacikulu ngati ici. 11  Koma nikukuuzani kuti ambili ocokela kum’maŵa na kumadzulo, adzabwela kudzakhala pa thebulo pamodzi na Abulahamu, Isaki, komanso Yakobo mu Ufumu wa kumwamba. 12  Koma ana a Ufumuwo adzaponyedwa kunja ku mdima. Kumeneko azikalila na kukukuta mano.” 13  Kenako Yesu anauza kapitawo wa asilikaliyo kuti: “Pita. Popeza waonetsa cikhulupililo, zimene wapempha zicitike.” Ndipo mu ola limenelo wanchito uja anacila. 14  Tsopano Yesu ataloŵa m’nyumba ya Petulo, anaona apongozi aakazi a Petulo ali cigonele cifukwa codwala malungo.* 15  Iye anagwila dzanja lawo, ndipo anacila malungowo, moti anauka n’kuyamba kumukonzela cakudya. 16  Koma madzulo anthu anamubweletsela anthu ambili ogwidwa na ziŵanda, ndipo iye anatulutsa mizimuyo na mawu cabe, komanso anacilitsa onse amene anali kudwala, 17  kuti mawu amene ananenedwa kudzela mwa mneneli Yesaya akwanilitsidwe akuti: “Iyeyo anacotsa matenda athu na kunyamula zoŵaŵa zathu.” 18  Yesu ataona kuti khamu la anthu lamuzungulila, analamula ophunzila ake kuti anyamuke n’kupita naye ku tsidya lina. 19  Tsopano mlembi wina anabwela n’kumuuza kuti: “Mphunzitsi, nikutsatilani kulikonse kumene mungapite.” 20  Koma Yesu anamuyankha kuti: “Nkhandwe zili na mapanga awo, ndipo mbalame za mumlengalenga zili na zisa, koma Mwana wa munthu alibe nyumba yake-yake.”* 21  Kenako wina mwa ophunzila ake anamuuza kuti: “Ambuye, niloleni coyamba nipite nikaike malilo a atate anga.” 22  Yesu anamuyankha kuti: “Pitiliza kunitsatila, aleke akufa aike akufa awo.” 23  Atakwela bwato, ophunzila ake anamutsatila. 24  Ndiyeno pa nyanjapo panauka namondwe woopsa! moti madzi anayamba kuloŵa m’bwatomo cifukwa ca kukula kwa mafunde; koma iye anali mtulo. 25  Kenako iwo anapita kukamuutsa n’kumuuza kuti: “Ambuye, tipulumutseni tikufa!” 26  Koma iye anawafunsa kuti: “N’cifukwa ciyani mukucita mantha conci, a cikhulupililo cocepa inu?” Kenako iye anauka n’kudzudzula mphepo na nyanjayo, ndipo panakhala bata lalikulu. 27  Poona izi, ophunzilawo anadabwa ndipo anati: “Kodi munthu ameneyu ni wotani? Ngakhale mphepo na nyanja zikumumvela!” 28  Yesu atafika kutsidya lina la nyanja m’cigawo ca Agadara, anakumana na amuna aŵili ogwidwa na ziŵanda akucokela ku manda.* Iwo anali aukali kwambili, moti panalibe munthu anali kulimba mtima kupitila njila imeneyo. 29  Pamenepo iwo anayamba kufuula kuti: “Mufuna ciyani kwa ife inu Mwana wa Mulungu? Kodi mwabwela kudzatizunza nthawi yoikika isanakwane?” 30  Capatali ndithu kucokela pamenepo, panali gulu la nkhumba zambili zimene zinali kudya. 31  Cotelo ziŵandazo zinayamba kumucondelela kuti: “Ngati mutitulutse, mutitumize tikaloŵe m’nkhumba izo.” 32  Ndipo Yesu anaziuza kuti: “Pitani!” Pamenepo ziŵandazo zinatuluka n’kupita kukaloŵa m’nkhumbazo. Zitatelo, nkhumbazo zinathamangila ku phompho mpaka kukagwela m’nyanja, ndipo zinafela momwemo. 33  Koma oŵetela nkhumbazo anathaŵa. Ataloŵa mu mzinda, anafotokozela anthu zonse zimene zinacitika, kuphatikizapo za amuna ogwidwa na ziŵanda aja. 34  Pamenepo anthu onse a mu mzindawo anapita kukakumana na Yesu, ndipo atamuona anamupempha kuti acoke m’dela lawo.

Mawu a m'Munsi

Mawu ake enieni, “kutentha thupi.”
Mawu ake enieni, “alibe kulikonse kumene angasamile mutu wake.”
Kapena kuti, “manda acikumbutso.”