Wolembedwa na Mateyo 26:1-75
-
Ansembe akonza ciwembu cakuti aphe Yesu (1-5)
-
Yesu athilidwa mafuta onunkhila (6-13)
-
Pasika wothela komanso kupelekedwa kwa Yesu (14-25)
-
Kukhazikitsidwa kwa Mgonelo wa Ambuye (26-30)
-
Yesu akambilatu kuti Petulo adzamukana (31-35)
-
Yesu apemphela m’munda wa Getsemane (36-46)
-
Yesu agwidwa (47-56)
-
Yesu azengedwa mlandu m’Khoti Yaikulu ya Ayuda (57-68)
-
Petulo akana Yesu (69-75)
26 Yesu atatsiliza kulankhula zinthu zonsezi, anauza ophunzila ake kuti:
2 “Inu mudziŵa kuti kwangotsala masiku aŵili kuti Pasika acitike, ndipo Mwana wa munthu adzam’peleka kuti amuphe pa mtengo.”
3 Pa nthawiyi, ansembe aakulu komanso akulu anasonkhana m’bwalo la mkati panyumba ya mkulu wa ansembe, dzina lake Kayafa.
4 Ndipo anapangana zakuti amugwile* Yesu mocenjela na kumupha.
5 Koma iwo anali kunena kuti: “Tisakamugwile pa cikondwelelo, kuopela kuti anthu angadzacite cipolowe.”*
6 Pamene Yesu anali ku Betaniya m’nyumba ya Simoni wakhate,
7 mayi wina anafika pafupi na Yesu atanyamula botolo la mwala wa alabasitala mmene munali mafuta odula onunkhila. Iye anayamba kuthila mafutawo pa mutu pa Yesu pamene anali kudya.
8 Ophunzila ake ataona zimenezi, anakwiya ndipo anati: “N’cifukwa ciyani akuwononga mafutawa?
9 Mafutawa akanagulitsidwa ndalama zambili, ndipo ndalamazo zikanapelekedwa kwa osauka.”
10 Yesu anadziŵa zimenezi ndipo anawafunsa kuti: “N’cifukwa ciyani mukumuvutitsa mayiyu? Zimene iyeyu wanicitila n’zabwino.
11 Pakuti osaukawo muli nawo nthawi zonse, koma ine simudzakhala nane nthawi zonse.
12 Mayiyu wathila mafuta onunkhilawa pathupi langa pokonzekela kuikidwa m’manda kwanga.
13 Ndithu nikukuuzani kuti, kulikonse kumene uthenga wabwinowu udzalalikidwa pa dziko lonse, anthu azikafotokozanso zimene mayiyu wacita pomukumbukila.”
14 Pambuyo pake mmodzi wa atumwi 12 aja wochedwa Yudasi Isikariyoti, anapita kwa ansembe aakulu
15 n’kuwafunsa kuti: “Mudzanipatsa ciyani nikamupeleka kwa inu?” Iwo anamulonjeza ndalama 30 za siliva.
16 Conco kucokela nthawi imeneyo, iye anayamba kufuna-funa mpata wabwino woti amupeleke.
17 Pa tsiku loyamba la cikondwelelo ca Mikate Yopanda Zofufumitsa, ophunzila a Yesu anafika kwa iye n’kumufunsa kuti: “Mufuna tikakukonzeleni kuti malo odyelako Pasika?”
18 Iye anati: “Pitani mu mzinda kwa Uje mukamuuze kuti, ‘Mphunzitsi akuti, “Nthawi yanga yoikika ili pafupi. Nidzacitila kunyumba kwako cikondwelelo ca Pasika pamodzi na ophunzila anga.”’”
19 Conco ophunzilawo anacita zimene Yesu anawalangiza, ndipo anakonza zonse zofunikila pa Pasika.
20 Nthawi ya madzulo, Yesu na ophunzila ake 12 aja anali kudya pa thebulo.
21 Pamene anali kudya Yesu anati: “Ndithu nikukuuzani kuti mmodzi wa inu anipeleka.”
22 Pomva cisoni kwambili na zimenezi, aliyense wa iwo anayamba kumufunsa kuti: “Ambuye, ndine kapena?”
23 Iye anayankha kuti: “Amene akusunsa nane pamodzi m’mbalemu ndiye anipeleke.
24 Zoonadi, Mwana wa munthu akupita, monga mmene Malemba amakambila za iye. Koma tsoka kwa munthu amene apeleke Mwana wa munthu! Cikanakhala bwino munthu ameneyo akanapanda kubadwa.”
25 Yudasi amene anatsala pang’ono kumupeleka anayankha kuti: “Mphunzitsi,* ningakhale ine kapena?” Yesu anamuyankha kuti: “Wakamba wekha.”
26 Akupitiliza kudya, Yesu anatenga mtanda wa mkate, ndipo atayamika anaunyema-nyema n’kuupeleka kwa ophunzila ake. Iye anati: “Aneni idyani. Mkate uwu ukuimila thupi langa.”
27 Ndiyeno anatenga kapu n’kuyamika, ndipo anapatsa ophunzila ake n’kuwauza kuti: “Imwani za m’kapuyi nonsenu.
28 Pakuti vinyoyu akuimila ‘magazi anga a cipangano,’ amene adzakhetsedwa kuti anthu ambili akhululukidwe macimo.
29 Koma nikukuuzani kuti: Sinidzamwanso cakumwa ciliconse cocokela ku mphesa kufikila tsiku limene nidzamwa cakumwa catsopano pamodzi na inu mu Ufumu wa Atate wanga.”
30 Pa mapeto pake, iwo atatsiliza kuimba nyimbo za citamando,* anapita ku Phili la Maolivi.
31 Kenako Yesu anawauza kuti: “Nonsenu muthaŵa n’kunisiya nekha usiku uno, cifukwa Malemba amanena kuti: ‘Nidzapha m’busa ndipo nkhosa zake zidzamwazikana.’
32 Koma nikadzaukitsidwa, nidzatsogola kupita ku Galileya inu musanafike kumeneko.”
33 Koma Petulo anamuyankha kuti: “Ngakhale ena onsewa atathaŵa n’kukusiyani, ine sinidzathaŵa!”
34 Yesu anamuuza kuti: “Ndithu nikukuuza kuti usiku wa lelo, iwe unikana katatu tambala asanalile.”
35 Petulo anayankha kuti: “Ngati n’kufa tifela pamodzi, ndipo siningakukaneni ngakhale pang’ono.” Ophunzila ena onsewo anakambanso cimodzi-modzi.
36 Kenako Yesu na ophunzila ake anafika pa malo ochedwa Getsemane, ndipo anawauza kuti: “Khalani pansi pompano, ine nipita uko kukapemphela.”
37 Popita kumeneko anatenga Petulo pamodzi na ana aŵili a Zebedayo. Ndipo anayamba kumva cisoni na kuvutika kwambili mumtima.
38 Kenako anawauza kuti: “Nili na cisoni cofa naco. Khalani pano ndipo mukhalebe maso pamodzi nane.”
39 Atapitako patsogolo pang’ono, anagwada mpaka nkhope yake pansi n’kuyamba kupemphela kuti: “Atate ngati n’kotheka, kapu iyi inipitilile. Osati mwa kufuna kwanga, koma mwa kufuna kwanu.”
40 Atabwelela kwa ophunzilawo anawapeza akugona, ndipo anafunsa Petulo kuti: “Kodi simungakhale maso pamodzi nane ngakhale kwa ola limodzi?
41 Khalanibe maso ndipo pitilizani kupemphela kuti musaloŵe m’mayeselo. Zoona mzimu ni wofunitsitsa,* koma thupi ni lofooka.”
42 Iye anapitanso kaciŵili kukapemphela ndipo anati: “Atate, ngati n’zosatheka kuti kapu iyi inipitilile mpaka n’tamwa ndithu, cifunilo canu cicitike.”
43 Atabwelelanso anawapeza akugona, cifukwa zikope zawo zinali zitalemela.
44 Conco anawasiya n’kupitanso kukapemphela kacitatu, akubweleza zinthu zimodzi-modzi.
45 Pambuyo pake anabwelelanso kwa ophunzilawo na kuwauza kuti: “Zoona pa nthawi ngati ino mukugona na kupumula! Onani! Ola lakuti Mwana wa munthu apelekedwe m’manja mwa ocimwa layandikila.
46 Nyamukani tiyeni tizipita. Onani! Wonipeleka uja ali pafupi.”
47 Ali mkati molankhula, Yudasi mmodzi wa Atumwi 12 aja anatulukila na khamu lalikulu la anthu, lotumidwa na ansembe aakulu komanso akulu. Anthuwo anali atanyamula malupanga na nkholi.
48 Pa nthawiyo, womupelekayo anali atawapatsa cizindikilo cakuti: “Amene nikam’psompsone ni ameneyo; mukamugwile.”
49 Atafika, Yudasi analunjika kwa Yesu n’kunena kuti: “Moni, Mphunzitsi!” Kenako anam’psompsona mwacikondi.
50 Koma Yesu anamufunsa kuti: “Bwanawe, wabwela kudzacita ciyani kuno?” Pamenepo anthuwo anafika pafupi n’kugwila Yesu na kumumanga.
51 Koma wina mwa amene anali na Yesu anasolola lupanga lake n’kutema nalo kapolo wa mkulu wa ansembe mpaka kumudula khutu.
52 Nthawi yomweyo Yesu anamuuza kuti: “Bwezela lupanga lako m’cimake, cifukwa onse onyamula lupanga adzafa na lupanga.
53 Kapena uganiza kuti siningapemphe Atate kuti anitumizile magulu oposa 12 a angelo nthawi yomwe ino?
54 Koma nikacita zimenezi, kodi Malemba amene anakambilatu kuti zotelezi ziyenela kucitika adzakwanilitsika bwanji?”
55 Pa nthawiyo Yesu anauza khamu la anthulo kuti: “N’cifukwa ciyani mwabwela kudzanigwila mutanyamula malupanga na nkholi, ngati kuti mukubwela kudzagwila wacifwamba? Tsiku lililonse n’nali kukhala m’kacisi kuphunzitsa koma simunanigwile.
56 Koma zonsezi zacitika kuti zolemba za aneneli zikwanilitsidwe.”* Kenako ophunzila ake onse anang’ondoka kuthaŵa n’kumusiya yekha.
57 Anthu amene anagwila Yesu aja anapita naye kwa Kayafa mkulu wa ansembe, kumene alembi na akulu anali atasonkhana.
58 Koma Petulo anamutsatilabe capatali ndithu, mpaka kukafika m’bwalo la kunyumba ya mkulu wa ansembe. Ataloŵa mkati anakhala pansi pamodzi na anchito a m’nyumbamo kuti aone zimene zicitike.
59 Pa nthawiyo, ansembe aakulu komanso onse mu Khoti Yaikulu ya Ayuda, anali kufuna-funa umboni wonama kuti amunamizile mlandu Yesu n’colinga cakuti amuphe.
60 Koma sanapeze umboni uliwonse ngakhale kuti kunabwela mboni zambili zonama. Pambuyo pake kunabwela mboni zina ziŵili.
61 Mbonizo zinati: “Munthu uyu anali kukamba kuti, ‘Ningathe kugwetsa kacisi wa Mulungu n’kumumanganso m’masiku atatu.’”
62 Mkulu wa ansembe atamva zimenezi anaimilila n’kumufunsa kuti: “Kodi suyankha ciliconse? Ukutipo ciyani pa zimene anthu awa akukuneneza?”
63 Koma Yesu anangokhala cete. Conco mkulu wa ansembeyo anamuuza kuti: “Nikukulumbilitsa pali Mulungu wamoyo, kuti utiuze ngati ndiwedi Khristu, Mwana wa Mulungu!”
64 Yesu anamuyankha kuti: “Inuyo mwanena nokha. Koma nikukuuzani kuti: Kuyambila tsopano, mudzaona Mwana wa munthu atakhala kudzanja lamanja lamphamvu, komanso akubwela pa mitambo ya kumwamba.”
65 Nthawi yomweyo mkulu wa ansembeyo anang’amba zovala zake zakunja, n’kunena kuti: “Wanyoza Mulungu! Kodi apa n’kufunanso umboni wina? Mwaona! Apa mwadzimvela nokha kuti akunyoza Mulungu.
66 Kodi inu mukutipo ciyani?” Iwo anayankha kuti: “Ameneyu ayenela kuphedwa ndithu.”
67 Kenako anamuthila mata kumaso na kum’menya makofi. Ena anamuwaza mbama kumaso,
68 n’kumanena kuti: “Iwe Khristu, lotela. Wakumenya ndani?”
69 Tsopano Petulo anakhala pansi panja m’bwalo lija, ndipo mtsikana wanchito anabwela kwa iye n’kunena kuti: “Inunso munali na Yesu wa ku Galileyayu!”
70 Koma iye anakana pamaso pa onse ndipo anati: “Sinizidziŵa zimene ukukamba.”
71 Atatuluka n’kupita ku kanyumba ka pageti, mtsikana winanso anamuzindikila n’kuuza amene anali pamenepo kuti: “Munthu uyu anali na Yesu Mnazareti.”
72 Apanso Petulo anakana mocita kulumbila, amvekele: “Ndithu munthu ameneyu sinimudziŵa!”
73 Patapita kanthawi pang’ono, amene anaimilila capafupi anabwela n’kuuza Petulo kuti: “Mosakayikila iwenso ndiwe mmodzi wa iwo, cifukwa kalankhulidwe kako kakuulula.”
74 Apa lomba iye anayamba kukana* na kulumbila kuti: “Nati munthu uyu ine sinimudziŵa iyayi!” Nthawi yomweyo tambala analila.
75 Ndipo Petulo anakumbukila mawu a Yesu aja akuti: “Iwe unikana katatu tambala asanalile.” Pamenepo anatuluka panja n’kuyamba kulila mwacisoni kwambili.
Mawu a m'Munsi
^ Kapena kuti, “amumange.”
^ Kapena kuti, “zaciwawa.”
^ Kapena kuti, “Rabi.” M’Ciheberi, Rabi ni dzina laulemu la mphunzitsi waciyuda.
^ Kapena kuti, “nyimbo zauzimu; masalimo.”
^ Kapena kuti, “mzimu ufuna.”
^ Kapena kuti, “malemba a aneneli akwanilitsidwe.”
^ Mawu ake enieni, “kudzitembelela.”