Wolembedwa na Mateyo 22:1-46

  • Fanizo la phwando la ukwati (1-14)

  • Mulungu na Kaisara (15-22)

  • Funso pa nkhani ya kuuka kwa akufa (23-33)

  • Malamulo aŵili aakulu kwambili (34-40)

  • Kodi Khristu ni mwana wa Davide? (41-46)

22  Yesu anawauzanso mafanizo ena. Anati: 2  “Ufumu wa kumwamba uli ngati mfumu imene inakonza phwando la ukwati wa mwana wake wamwamuna. 3  Ndipo inatuma akapolo ake kuti akaitane anthu oitanidwa ku phwando la ukwatilo, koma iwo anakana. 4  Anatumanso akapolo ena n’kuwauza kuti, ‘Kauzeni oitanidwa aja kuti: “Taonani! Nakonza cakudya ca masana, napha ng’ombe zanga na nyama zanga zonenepa, ndipo zonse zakonzedwa kale. Bwelani ku phwando la ukwati.”’ 5  Koma oitanidwawo sanalabadile ndipo anacoka, wina anapita ku munda kwake, wina ku malonda ake. 6  Koma enawo anagwila akapolo aja, ndipo anawazunza n’kuwapha. 7  “Pamenepo mfumu ija inakwiya koopsa, ndipo inatuma asilikali ake kukapha anthu amene anapha akapolo ake aja n’kutentha mzinda wawo. 8  Kenako anauza akapolo ake kuti, ‘Phwando la ukwati lakonzedwa, koma amene anaitanidwa aja sanali oyenela. 9  Conco, pitani m’misewu yotulukila mu mzinda uno, mukaitane aliyense amene mum’peze kuti abwele ku phwando la ukwatili.’ 10  Conco akapolowo anapita m’misewu na kusonkhanitsa anthu onse amene anapeza, oipa na abwino omwe. Ndipo cipinda cocitilamo phwando la ukwatilo cinadzala na anthu olandila cakudya. 11  “Mfumu ija italoŵa m’cipindamo poyendela oitanidwawo, inaona munthu wina amene sanavale covala ca ukwati. 12  Mfumuyo inamufunsa kuti, ‘Bwanawe, waloŵa bwanji muno popanda covala ca ukwati?’ Iye anasoŵa cokamba. 13  Basi mfumuyo inauza atumiki ake kuti, ‘M’mangeni manja na miyendo na kum’ponya kunja ku mdima. Kumeneko azikalila na kukukuta mano.’ 14  “Pakuti oitanidwa ni ambili koma osankhidwa ni oŵelengeka.” 15  Pambuyo pake Afarisi anapita kukapangana zakuti amutape m’kamwa Yesu. 16  Conco iwo anamutumizila ophunzila awo pamodzi na a cipani ca Herode. Iwo anati: “Mphunzitsi, tidziŵa kuti mumakamba zoona na kuphunzitsa njila ya Mulungu m’coonadi, komanso simukondela cifukwa simuyang’ana maonekedwe a anthu. 17  Ndiye tiuzeni, muganiza bwanji? Kodi n’kololeka* kupeleka msonkho kwa Kaisara kapena ayi?” 18  Koma Yesu podziŵa colinga cawo coipa anati: “Onyenga inu, n’cifukwa ciyani mukuniyesa? 19  Nionetseni khobili la msonkhowo.” Iwo anamubweletsela khobili la dinari. 20  Kenako iye anawafunsa kuti: “Kodi cithunzi ici na mawu awa n’zandani?” 21  Iwo anayankha kuti: “Ni za Kaisara.” Ndiyeno iye anawauza kuti: “Conco pelekani zinthu za Kaisara kwa Kaisara, koma za Mulungu kwa Mulungu.” 22  Atamva zimenezi anadabwa kwambili ndipo anamusiya n’kucoka. 23  Pa tsiku limenelo, Asaduki amene amati kulibe kuuka kwa akufa, anabwela n’kumufunsa kuti: 24  “Mphunzitsi, Mose anati: ‘Mwamuna akamwalila wopanda ana, m’bale wake ayenela kukwatila mkazi wamasiyeyo, n’kubelekela m’bale wake uja ana.’ 25  Lomba panali amuna 7 apacibale. Woyamba anakwatila kenako anamwalila. Koma popeza analibe ana, mkazi uja anakwatiwa na m’bale wa mwamuna wake. 26  Zinacitika cimodzimodzi kwa waciŵili na wacitatu mpaka kwa onse 7. 27  Pothela pake mkazi uja nayenso anamwalila. 28  Ndiye pamene akufa adzauka, kodi mkaziyo adzakhala wa ndani popeza onse 7 anamukwatilapo?” 29  Yesu anawayankha kuti: “Mukulakwitsa, cifukwa simudziŵa Malemba kapena mphamvu za Mulungu; 30  Pakuti pa kuuka kwa akufa amuna sadzakwatila, ndipo akazi sadzakwatiwa, koma adzakhala ngati angelo akumwamba. 31  Ponena za kuuka kwa akufa, kodi simunaŵelenge zimene Mulungu anakuuzani pamene anati: 32  ‘Ine ndine Mulungu wa Abulahamu, Mulungu wa Isaki komanso Mulungu wa Yakobo? Iye si Mulungu wa akufa, koma wa anthu amoyo.” 33  Khamulo litamva zimenezi, linadabwa kwambili na kaphunzitsidwe kake. 34  Afarisi atamva kuti Yesu anawasoŵetsa conena Asaduki, anasonkhana pamodzi n’kubwela kwa iye. 35  Ndipo mmodzi wa iwo, wodziŵa Cilamulo, anamuyesa mwa kumufunsa kuti: 36  “Mphunzitsi, kodi lamulo lalikulu kwambili m’Cilamulo ni liti?” 37  Iye anamuyankha kuti: “‘Uzikonda Yehova Mulungu wako na mtima wako wonse, moyo wako wonse, na maganizo ako onse.’ 38  Ili ndilo lamulo lalikulu kwambili komanso loyamba. 39  Laciŵili lofanana nalo ni ili: ‘Uzikonda mnzako mmene umadzikondela wekha.’ 40  Cilamulo conse komanso zolemba za aneneli zagona pa malamulo aŵili amenewa.” 41  Ndiyeno Afarisi aja atasonkhana pamodzi, Yesu anawafunsa kuti: 42  “Muganiza bwanji za Khristu? Kodi ni mwana wa ndani?” Iwo anamuyankha kuti: “Wa Davide.” 43  Iye anawafunsanso kuti: “Nanga n’cifukwa ciyani Davide mouzilidwa anamuchula kuti Ambuye, pamene anati 44  ‘Yehova anauza Ambuye wanga kuti: “Khala ku dzanja langa lamanja, kufikila nitaika adani ako kunsi kwa mapazi ako”’? 45  Ngati Davide anamuchula kuti Ambuye, ndiye akhala bwanji mwana wake?” 46  Koma palibe anatha kumuyankha, ndipo kucokela tsiku limenelo palibe analimba mtima kumufunsanso mafunso.

Mawu a m'Munsi

Kapena kuti, “kodi n’koyenela.”