Wolembedwa na Maliko 9:1-50

  • Kusandulika kwa Yesu (1-13)

  • Kamnyamata kogwidwa na ciŵanda kacilitsidwa (14-29)

    • Zinthu zonse n’zotheka kwa munthu wacikhulupililo (23)

  • Yesu akambilatunso za imfa yake (30-32)

  • Ophunzila akangana zakuti wamkulu ndani (33-37)

  • Aliyense amene satsutsana nafe ali ku mbali yathu (38-41)

  • Zopunthwitsa (42-48)

  • “Khalani na mcele mwa inu” (49, 50)

9  Iye anawauzanso kuti: “Ndithu nikukuuzani kuti pali ena pano amene sadzalaŵa imfa ngakhale pang’ono, mpaka coyamba ataona Ufumu wa Mulungu utayamba kulamulila.”  Patapita masiku 6, Yesu anatenga Petulo, Yakobo, na Yohane n’kukwela nawo m’phili lalitali kwaokha-okha. Kumeneko, iye anasandulika pamaso pawo.  Zovala zake zakunja zinayamba kunyezimila n’kuyela mbee, kuposa mmene wocapa zovala aliyense pa dziko lapansi angaziyeletsele.  Komanso Eliya na Mose anaonekela kwa iwo, akulankhula na Yesu.  Tsopano Petulo anauza Yesu kuti: “Mphunzitsi,* zili bwino kuti ife tizikhala pompano. Ngati mufuna, ningakhome matenti atatu pano. Ina yanu, ina ya Mose, inanso ya Eliya.”  Iye anakamba zimenezi posoŵa cocita, cifukwa onse atatu anacita mantha kwambili.  Ndiyeno kunacita mtambo, ndipo unawaphimba. Kenako mu mtambomo munamveka mawu akuti: “Uyu ni Mwana wanga wokondeka. Muzimumvela.”  Ndiyeno iwo atayang’ana-yang’ana anangoona kuti palibenso aliyense amene ali nawo, kupatulapo Yesu.  Pamene anali kutsika m’philimo, Yesu anawalamula mwamphamvu kuti asauze aliyense zimene anaona, mpaka Mwana wa munthu ataukitsidwa kwa akufa. 10  Iwo anasungadi mawu amenewa mumtima,* koma anali kukambilana tanthauzo la kuuka kwa akufa kumeneku. 11  Ndipo anayamba kumufunsa kuti: “N’cifukwa ciyani alembi amakamba kuti Eliya ayenela kubwela coyamba?” 12  Iye anawayankha kuti: “Eliya adzabweladi coyamba ndipo adzabwezeletsa zinthu zonse. Koma n’cifukwa ciyani Malemba amakamba kuti Mwana wa munthu ayenela kukumana na mavuto ambili komanso kucitidwa cipongwe? 13  Koma nikukuuzani kuti Eliya anabwela kale, ndipo anamucita ciliconse cimene anali kufuna monga mmene Malemba amanenela za iye.” 14  Atafika kumene kunali ophunzila ena aja, anaona khamu lalikulu la anthu litawazungulila, ndipo panali alembi amene anali kukangana nawo. 15  Koma anthu onsewo atangomuona anadabwa kwambili, ndipo anam’thamangila kuti akam’patse moni. 16  Conco iye anawafunsa kuti: “Kodi mukukangana nawo ciyani?” 17  Mmodzi m’khamulo anamuyankha nati: “Mphunzitsi, nabweletsa mwana wanga kwa inu, cifukwa ali na mzimu umene umamulepheletsa kulankhula. 18  Nthawi zonse mzimuwo ukamugwila, umamugwetsela pansi. Ndipo amacita thovu kukamwa, n’kumakukuta mano ndipo amafooka. N’napempha ophunzila anu kuti autulutse koma alephela.” 19  Poyankha iye anawauza kuti: “Inu m’badwo wopanda cikhulupililo, nikhalabe nanu mpaka liti? Kodi nikupilileni mpaka liti? M’bweletseni kuno.” 20  Conco anamubweletsa kwa iye. Koma mzimuwo utangoona Yesu, unam’gwetsela pansi mwanayo ndipo anayamba kupalapata. Kenako anayamba kukunkhulika, uku akucita thovu kukamwa. 21  Ndiyeno Yesu anafunsa tate wa mwanayo kuti: “Kodi izi zakhala zikumucitikila kwa nthawi yaitali bwanji?” Tateyo anayankha kuti: “Kuyambila ali wamng’ono, 22  ndipo nthawi zambili umamugwetsela pa moto komanso pa madzi kuti umuphe. Koma ngati mungathe kucitapo kanthu, timveleni cifundo ndipo mutithandize.” 23  Yesu anamuuza kuti: “N’cifukwa ciyani mukukamba kuti, ‘Ngati mungathe’? Zinthu zonse n’zotheka ndithu kwa munthu amene ali na cikhulupililo.” 24  Nthawi yomweyo, tate wa mwanayo anafuula amvekele: “Cikhulupililo nili naco! N’thandizeni kulimbitsa cikhulupililo canga!” 25  Tsopano Yesu poona kuti khamu la anthu likuthamangila kwa iye, anakalipila mzimu wonyansawo nati: “Iwe mzimu wolepheletsa kulankhula komanso wogonthetsa munthu, nikukulamula kuti, tuluka ndipo usadzaloŵenso mwa iye!” 26  Mzimuwo unafuula mokweza na kucititsa mwanayo kupalapata kwambili. Kenako unatuluka. Koma mwanayo anangokhala ngati wafa, moti anthu ambili anali kunena kuti: “Wamwalila!” 27  Koma Yesu anamugwila dzanja mwanayo n’kumuimilitsa, ndipo anaimilila. 28  Ndiyeno ataloŵa m’nyumba, ophunzila ake anamufunsa ali okha kuti: “N’cifukwa ciyani ife tinalephela kutulutsa ciŵanda cija?” 29  Iye anawayankha kuti: “Ciŵanda cotele sicingatuluke popanda pemphelo.” 30  Iwo anacoka kumeneko n’kudutsa m’Galileya. Koma sanafune kuti aliyense adziŵe kumene ali. 31  Pakuti iye anali kuphunzitsa ophunzila ake na kuwauza kuti: “Mwana wa munthu adzapelekedwa m’manja mwa anthu, ndipo iwo adzamupha. Koma ngakhale adzamuphe, iye adzaukitsidwa pambuyo pa masiku atatu.” 32  Koma iwo sanamvetse tanthauzo la mawu akewo, ndipo anaopa kumufunsa. 33  Ndiyeno anafika ku Kaperenao. Ndipo ali m’nyumba anawafunsa kuti: “Munali kukangana ciyani m’njila?” 34  Koma iwo anangokhala cete, cifukwa m’njila anali kukangana pa nkhani yakuti wamkulu ndani. 35  Conco anakhala pansi n’kuitana ophunzila ake 12 aja, ndipo anawauza kuti: “Ngati munthu afuna kukhala woyamba, akhale wothela pa onse komanso mtumiki wa onse.” 36  Kenako anatenga mwana wamng’ono n’kumuimika pakati pawo, ndipo anaika manja ake pa mapewa a mwanayo n’kuwauza kuti: 37  “Aliyense wolandila mwana wamng’ono ngati uyu cifukwa ca dzina langa, walandilanso ine. Ndipo aliyense wolandila ine, sanalandile ine nekha, koma walandilanso Iye amene ananituma.” 38  Ndiyeno Yohane anamuuza kuti: “Mphunzitsi, ife tinaona winawake akutulutsa ziŵanda m’dzina lanu, ndipo tamuletsa cifukwa sayenda nafe.” 39  Koma Yesu anati: “Musamuletse, cifukwa palibe aliyense yemwe angacite nchito yamphamvu m’dzina langa, amene mwamsanga angasinthe n’kuyamba kunena zoipa za ine. 40  Cifukwa aliyense amene satsutsana nafe, ali ku mbali yathu. 41  Ndipo aliyense wokupatsani kapu ya madzi kuti mumwe cifukwa cakuti ndinu otsatila a Khristu, ndithu nikukuuzani, iye sadzalephela konse kulandila mphoto yake. 42  Koma aliyense wopunthwitsa mmodzi wa ana aang’ono awa amene ali na cikhulupililo, cingakhale bwino kwambili atam’mangilila cimwala camphelo m’khosi cimene bulu amaguza na kum’ponya m’nyanja. 43  “Ngati dzanja lako limakupunthwitsa, ulidule. Ni bwino kuti ukalandile moyo* ulibe ciwalo cimodzi, kusiyana n’kuti ukapite na manja onse aŵili ku Gehena,* ku moto wosazimitsika. 44 * —— 45  Ndipo ngati phazi lako limakupunthwitsa, ulidule. Ni bwino kuti ukalandile moyo uli wolemala, kusiyana n’kuti ukaponyedwe ku Gehena* uli na mapazi onse aŵili. 46 * —— 47  Komanso ngati diso lako limakupunthwitsa, ulikolowole. Ni bwino kuti ukaloŵe mu Ufumu wa Mulungu uli na diso limodzi, kusiyana n’kuti ukaponyedwe ku Gehena* uli na maso onse aŵili, 48  kumene mphutsi sizikufa komanso moto suzima. 49  “Monga mmene mcele umathilidwila, aliyense wa anthuwo adzathilidwa moto. 50  Mcele ni wabwino. Koma ngati mcele ungathe mphamvu yake, kodi mphamvuyo mungaibwezeletse na ciyani? Khalani na mcele mwa inu, ndipo sungani mtendele pakati panu.”

Mawu a m'Munsi

Kapena kuti, “Rabi.” M’Ciheberi, Rabi ni dzina laulemu la mphunzitsi waciyuda.
Kamasulidwe kena, “Iwo sanauzeko aliyense nkhaniyo.”
Onani mawu a m’munsi pa Mateyo 18:8.
Mawu a pa vesiyi amapezeka m’ma Baibo ena, koma sapezeka m’mipukutu yosiyana-siyana yodalilika yamakedzana ya Cigiriki.
Mawu a pa vesiyi amapezeka m’ma Baibo ena, koma sapezeka m’mipukutu yosiyana-siyana yodalilika yamakedzana ya Cigiriki.