Wolembedwa na Maliko 5:1-43
5 Ndiyeno iwo anafika ku tsidya lina la nyanja m’cigawo ca Agerasa.
2 Yesu atangotsika m’bwato anakumana na munthu wina wogwidwa na mzimu wonyansa akucokela ku manda.*
3 Iye anali kukonda kukhala ku mandako. Kumbuyo konseko, panalibe aliyense amene anakwanitsa kumumanga ngakhale na cheni koma iye osadula.
4 Nthawi zambili anali kumumanga m’matangadza komanso na macheni. Koma anali kudula macheniwo na kuthyola matangadzawo, moti panalibe aliyense amene anali na mphamvu zomugonjetsa.
5 Nthawi zonse usana na usiku anali kufuula ali ku manda komanso m’mapili, ndipo anali kudziceka-ceka na miyala.
6 Koma ataona Yesu capatali anamuthamangila na kumuŵelamila.
7 Ndiyeno anafuula mwamphamvu, amvekele: “Mufuna ciyani kwa ine, inu Yesu, Mwana wa Mulungu Wapamwambamwamba? Nikukulumbilitsani pali Mulungu kuti musanizunze ayi.”
8 Anafuula motelo cifukwa Yesu anali kuuza mzimuwo kuti: “Tuluka mwa munthuyu iwe mzimu wonyansa.”
9 Koma Yesu anafunsa mzimuwo kuti: “Dzina lako ndani?” Mzimuwo unayankha kuti: “Dzina langa ndine Khamu, cifukwa ndife ambili.”
10 Ndipo unapitiliza kucondelela Yesu kuti asatumize mizimuyo kutali na delalo.
11 Pa nthawiyi, nkhumba zambili zinali kudya kumeneko m’mbali mwa phili.
12 Conco mizimuyo inamucondelela kuti: “Mutitumize m’nkhumba izo, tikaloŵe mmenemo.”
13 Ndipo anailola. Pamenepo mizimu yonyansa ija inatuluka n’kupita kukaloŵa m‘nkhumbazo, ndipo nkhumbazo zinathamangila ku phompho mpaka kukagwela m’nyanja. Nkhumbazo zinalipo pafupifupi 2,000, ndipo zinamila m’nyanjamo.
14 Oŵetela nkhumbazo anathaŵa n’kukafotokozela anthu mu mzinda na m’midzi, ndipo anthuwo anabwela kudzaona zimene zinacitika.
15 Conco anafika kwa Yesu, ndipo anaona munthu amene anali wogwidwa na ciŵanda uja, amene poyamba anali na khamu la mizimu yonyansa. Iwo atamuona ali khale komanso atavala, ndiponso maganizo ake ali bwino-bwino, anacita mantha.
16 Komanso amene anaona zimene zinacitikazo, anafotokozela anthuwo zimene zinacitikila munthu wogwidwa na ziŵandayo, ndiponso nkhumba zija.
17 Cotelo anthuwo anayamba kumucondelela Yesu kuti acoke m’dela lawo.
18 Tsopano pamene Yesu anali kukwela bwato, munthu amene anali wogwidwa na ziŵanda uja anayamba kumucondelela kuti apite naye.
19 Koma Yesu sanamulole. M’malo mwake anamuuza kuti: “Pita ku nyumba ya acibale ako, ndipo ukawauze zonse zimene Yehova wakucitila, komanso cifundo cimene wakuonetsa.”
20 Cotelo munthu uja anapita, ndipo anayamba kufalitsa mu Dekapoli* zonse zimene Yesu anamucitila, ndipo anthu onse anadabwa kwambili.
21 Yesu atawolokelanso ku tsidya lina la nyanja pa bwato, khamu lalikulu la anthu linasonkhana kwa iye, apo n’kuti iye ali m’mbali mwa nyanjayo.
22 Mmodzi wa atsogoleli a sunagoge dzina lake Yairo anabwela. Ataona Yesu anagwada pa mapazi ake.
23 Kenako iye anamucondelela mobweleza-bweleza kuti: “Mwana wanga wamkazi wamng’ono akudwala kwakaya-kaya.* Conde tiyeni mukaike manja anu pa iye kuti acile n’kukhala na moyo.”
24 Pamenepo Yesu anapita naye, ndipo khamu lalikulu la anthu linali kumutsatila na kumupanikiza.
25 Lomba panali mayi wina amene anali kudwala matenda otaya magazi kwa zaka 12.
26 Madokotala ambili anamucititsa kuti avutike ngako.* Iye anawononga cuma cake conse koma osacila. M’malo mwake, matendawo anali kungokulila-kulila.
27 Atamva mbili ya Yesu, analoŵa m’gulu la anthu n’kupita kumbuyo kwake. Kenako anagwila covala cake cakunja,
28 cifukwa mu mtima anali kunena kuti: “Nikangogwila covala cake cakunja nicila ndithu.”
29 Nthawi yomweyo analeka kutaya magazi, ndipo anamva m’thupi mwake kuti wacila matenda ake aakuluwo.
30 Nthawi yomweyo Yesu anadziŵa kuti mphamvu yatuluka mwa iye, ndipo anaceuka m’gululo n’kufunsa kuti: “Ndani wagwila malaya anga akunja?”
31 Koma ophunzila ake anamuyankha kuti: “Inu mukuona kuti gulu lonseli likukupanikizani, ndiye mukufunsilanji kuti, ‘Ndani wanigwila?’”
32 Koma iye anali kuyang’ana-yang’ana kuti aone amene wacita zimenezi.
33 Mayiyo podziŵa zimene zamucitikila, anacita mantha n’kuyamba kunjenjemela. Ndipo anapita kwa Yesu n’kugwada pamaso pake, n’kumuuza zoona zonse.
34 Kenako iye anauza mayiyo kuti: “Mwanawe, cikhulupililo cako cakucilitsa. Pita mu mtendele, ndipo matenda ako aakuluwo atheletu.”
35 Ali mkati molankhula, amuna ena ocokela ku nyumba ya mtsogoleli uja wa sunagoge anabwela na kumuuza kuti: “Mwana wanu wamwalila! Mulekeni Mphunzitsiyu osamuvutitsa.”
36 Koma Yesu atamva zimene iwo anali kukamba, anauza mtsogoleli wa sunagogeyo kuti: “Usacite mantha, ungokhala na cikhulupililo.”
37 Koma pa nthawiyi sanalolenso aliyense kumutsatila kupatulapo Petulo, Yakobo, na Yohane m’bale wake wa Yakobo.
38 Conco anafika ku nyumba ya mtsogoleli uja wa sunagoge, ndipo anamva ciphokoso ca anthu akulila na kubuma* kwambili.
39 Yesu ataloŵa anawauza kuti: “N’cifukwa ciyani mukulila na kubuma motele? Mwanayu sanamwalile koma wagona.”
40 Anthuwo atamva zimenezi anayamba kumuseka monyodola. Koma atawatulutsa onse, anatenga tate na mayi a mwanayo komanso anthu amene anali naye, n’kuloŵa kumene kunali mwanayo.
41 Kenako, anagwila dzanja la mwanayo n’kumuuza kuti: “Talita kumi,” mawu amene akamasulidwa amatanthauza kuti: “Kamtsikanawe, nikukuuza kuti, uka!”
42 Ndipo nthawi yomweyo, mtsikanayo anauka n’kuyamba kuyenda. (Mtsikanayo anali na zaka 12.) Pamenepo anthuwo anakondwela ngako.
43 Koma mobweleza-bweleza anawalamula* kuti asauzeko ena zimenezo. Kenako anawauza kuti amupatse cakudya mwanayo.
Mawu a m'Munsi
^ Kapena kuti, “manda acikumbutso.”
^ Kapena kuti, “Cigawo ca Mizinda 10.”
^ Kapena kuti, “watsala pangʼono kufa.”
^ Kapena kuti, “anamucititsa kuti amve zoŵaŵa zambili.”
^ Kutanthauza, “kulila kwa gulu la anthu pa malilo.”
^ Kapena kuti, “anawalamula mwamphamvu.”