Wolembedwa na Maliko 12:1-44
12 Ndiyeno anayamba kukamba nawo mwa mafanizo kuti: “Munthu wina analima munda wa mpesa n’kumanga mpanda kuzungulila mundawo. Ndipo anakumba dzenje lopondelamo mphesa na kumanga nsanja. Kenako anausiya m’manja mwa alimi n’kupita ku dziko lina.
2 Nyengo yokolola itakwana, iye anatuma kapolo wake kwa alimiwo kuti akatengeko zina mwa zipatso za m’munda wa mpesawo.
3 Koma iwo anamugwila n’kumumenya, ndipo anamubweza cimanjamanja.
4 Iye anatumanso kapolo wina kwa iwo, ndipo ameneyo anamutema m’mutu na kumucita zacipongwe.
5 Anatumanso wina, ndipo ameneyo anamupha. Komanso anatuma ena ambili, ndipo ena a iwo anawamenya, ena anawapha.
6 Ndiyeno anatsala na mmodzi yekha woti atume, mwana wake wokondeka. Pothela, iye anatuma mwanayo n’kunena kuti, ‘Mwana wangayu akamulemekeza.’
7 Koma alimiwo anayamba kukambilana kuti, ‘Eya! Uyu ndiye wolandila coloŵa. Bwelani, tiyeni timuphe ndipo coloŵaci cidzakhala cathu.’
8 Conco iwo anamugwila n’kumupha. Kenako anamutayila kunja kwa munda wa mpesawo.
9 Kodi mwinimundayo adzacita ciyani? Adzabwela n’kupha alimiwo ndipo adzapeleka mundawo kwa ena.
10 Kodi simunaŵelengepo zimene lemba limanena? Paja limati: ‘Mwala umene omanga anaukana, wakhala mwala wa pakona wofunika kwambili.*
11 Umenewu wacokela kwa Yehova, ndipo ni wodabwitsa m’maso mwathu’.”
12 Atamva zimenezi anafuna kumugwila,* cifukwa anadziŵa kuti iye anali kunena za iwo pokamba fanizo limeneli. Koma poopa khamu la anthu, anangomuleka n’kucokapo.
13 Kenako anamutumizila ena mwa Afarisi komanso a cipani ca Herode kuti akamutape m’kamwa.
14 Iwo atafika, anamuuza kuti: “Mphunzitsi, tidziŵa kuti mumakamba zoona komanso simukondela cifukwa simuyang’ana maonekedwe a anthu, koma mumaphunzitsa njila ya Mulungu m’coonadi. Kodi n’kololeka* kupeleka msonkho kwa Kaisara kapena ayi?
15 Kodi tiyenela kupeleka kapena ayi?” Atazindikila cinyengo cawo, anawauza kuti: “N’cifukwa ciyani mukuniyesa? Bweletsani khobili la Dinari nilione.”
16 Iwo anamubweletsela khobili limodzi, ndipo iye anawafunsa kuti: “Kodi cithunzi ici na mawu awa ni za ndani?” Iwo anayankha kuti: “Ni za Kaisara.”
17 Ndiyeno Yesu anati: “Pelekani zinthu za Kaisara kwa Kaisara, koma za Mulungu kwa Mulungu.” Ndipo anthuwo anadabwa naye kwambili.
18 Tsopano Asaduki amene amati kulibe kuuka kwa akufa anabwela n’kumufunsa kuti:
19 “Mphunzitsi, Mose anatilembela kuti ngati munthu wamwalila n’kusiya mkazi koma sanabeleke naye mwana, m’bale wake wa munthuyo ayenela kukwatila mkazi wamasiyeyo na kumubelekela ana m’bale wake uja.
20 Lomba panali amuna 7 a pacibale. Woyamba anakwatila mkazi, koma anamwalila asanabeleke naye mwana mkaziyo.
21 Waciŵili anamukwatila mkaziyo, koma nayenso anamwalila asanabeleke naye mwana. N’zimenenso zinacitikila mwamuna wacitatu.
22 Ndipo amuna onse 7 anamwalila osabeleka naye mwana. Pothela pake, mkazi uja nayenso anamwalila.
23 Pamene akufa adzauka, kodi mkaziyo adzakhala wa ndani popeza onse 7 anamukwatilapo?”
24 Yesu anawauza kuti: “Simudziŵa Malemba kapena mphamvu za Mulungu, ndiye cifukwa cake mukuganiza molakwika.
25 Pakuti anthu akadzauka kwa akufa, amuna sadzakwatila ndipo akazi sadzakwatiwa koma adzakhala ngati angelo a kumwamba.
26 Koma pa nkhani yakuti akufa adzauka, kodi simunaŵelenge m’buku la Mose pa nkhani yokamba za citsamba ca minga, kuti Mulungu anamuuza kuti: ‘Ine ndine Mulungu wa Abulahamu, Mulungu wa Isaki, komanso Mulungu wa Yakobo’?
27 Iye si Mulungu wa akufa ayi, koma wa anthu amoyo. Maganizo anu ni olakwika kwambili.”
28 Mmodzi wa alembi amene anabwela anawamva akutsutsana. Podziŵa kuti Yesu anawayankha bwino Asadukiwo, iye anamufunsa kuti: “Kodi lamulo loyamba* pa malamulo onse ni liti?”
29 Yesu anamuyankha kuti: “Lamulo loyamba n’lakuti, ‘Mvelani inu Aisiraeli, Yehova Mulungu wathu ni Yehova mmodzi basi.
30 Ndipo uzikonda Yehova Mulungu wako na mtima wako wonse, moyo wako wonse, maganizo ako onse, na mphamvu zako zonse.’
31 Laciŵili ni ili, ‘Uzikonda munthu mnzako mmene umadzikondela wekha.’ Palibe lamulo lina lalikulu kuposa amenewa.”
32 Mlembiyo anamuuza kuti: “Mphunzitsi mwakamba bwino mogwilizana na coonadi, ‘Iye ni mmodzi basi ndipo palibenso wina kupatulapo iye.’
33 Ndipo kumukonda na mtima wathu wonse, nzelu zathu zonse, na mphamvu zathu zonse komanso kukonda munthu mnzathu mmene timadzikondela n’kofunika kwambili. Zimenezi zimaposa nsembe zonse zonyeketsa zathunthu na nsembe zina.”
34 Yesu ataona kuti mlembiyo wayankha mwanzelu anamuuza kuti: “Suli kutali na Ufumu wa Mulungu.” Ndipo palibe amene analimbanso mtima kumufunsa mafunso.
35 Komabe, pamene Yesu anali kuphunzitsa m’kacisi ananena kuti: “N’cifukwa ciyani alembi amakamba kuti Khristu ni mwana wa Davide?
36 Motsogoleledwa na mzimu woyela, Davide iyemwini anati, ‘Yehova anauza Ambuye wanga kuti: “Khala ku dzanja langa lamanja kufikila n’taika adani ako kunsi kwa mapazi ako.”’
37 Ngati Davideyo akumucha Ambuye, zitheka bwanji iye kukhala mwana wake?”
Ndipo khamu lalikulu la anthu linali kumumvetsela mokondwela.
38 Pophunzitsa, Yesu anakambanso kuti: “Samalani na alembi amene amafuna kumayendayenda atavala mikanjo, amenenso amafuna kupatsidwa moni m’misika.
39 Iwo amafunanso kukhala pa mipando yakutsogolo* m’masunagoge, komanso pamalo olemekezeka kwambili pa cakudya camadzulo.
40 Amalanda cuma ca akazi* amasiye komanso amapeleka mapemphelo atali-atali pofuna kudzionetsela.* Amenewa adzalandila cilango coŵaŵa* kwambili.”
41 Ndiyeno anakhala pansi atayang’ana kumene kunali coponyamo zopeleka. Iye anayamba kuona mmene gulu la anthu linali kuponyela ndalama mmenemo. Ndipo anthu ambili olemela anali kuponyamo makobili ambili.
42 Kenako kunabwela mkazi wamasiye wosauka n’kuponyamo tumakobili tuŵili tocepa mphamvu kwambili.
43 Conco iye anaitana ophunzila ake n’kuwauza kuti: “Ndithu nikukuuzani, mayi wamasiye wosaukayu waponya zambili kuposa ena onse amene aponya ndalama moponya zopelekamu.
44 Pakuti onsewa aponya zimene atapa pa zoculuka zimene ali nazo, koma mayiyu ngakhale kuti ni wosauka, wapeleka zonse zimene anali nazo, zonse zimene zikanamuthandiza pa moyo wake.”
Mawu a m'Munsi
^ Mawu ake enieni, “mutu wa kona.”
^ Kapena kuti, “kumumanga.”
^ Kapena kuti, “n’coyenela.”
^ Kapena kuti, “lofunika kwambili.”
^ Kapena kuti, “yabwino kwambili.”
^ Mawu ake enieni, “Amadya nyumba za akazi.”
^ Kapena kuti, “mwaciphamaso.”
^ Kapena kuti, “colema.”