Macitidwe a Atumwi 14:1-28
14 Tsopano Paulo ndi Baranaba ali ku Ikoniyo analowa mu sunagoge wa Ayuda, ndipo analankhula bwino kwambili cakuti Ayuda komanso Agiriki ambili anakhala okhulupilila.
2 Koma Ayuda amene sanakhulupilile anatuntha anthu a mitundu ina ndi kuwasokoneza kuti aukile abalewo.
3 Cotelo kwa nthawi yaitali, analankhula molimba mtima cifukwa ca mphamvu ya Yehova. Iye anacitila umboni mawu a cisomo cake mwa kulola ophunzilawo kucita zizindikilo ndi zodabwitsa.
4 Koma khamu la anthu mu mzindawo linagawikana. Ena anali kumbali ya Ayuda, pamene ena anali kumbali ya atumwi.
5 Ndiyeno anthu a mitundu ina, komanso Ayuda pamodzi ndi olamulila awo, anakonza zakuti awacite cipongwe ndi kuwaponya miyala.
6 Koma atumwiwo anadziwitsidwa, ndipo anathawila mʼmizinda ya Lukaoniya, Lusitara, Debe, ndi mʼmadela ozungulila.
7 Kumeneko anapitiliza kulengeza uthenga wabwino.
8 Ku Lusitara, kunali munthu wina wolemala miyendo amene anali khale pansi. Munthuyu anabadwa wolemala ndipo anali asanayendepo.
9 Iye anali kumvetsela pamene Paulo anali kulankhula. Paulo anamuyangʼanitsitsa munthuyo, ndipo anaona kuti ali ndi cikhulupililo cakuti angacilitsidwe.
10 Conco Paulo mokweza mawu anati: “Imilila!” Atatelo, munthuyo analumpha nʼkuyamba kuyenda.
11 Khamu la anthu litaona zimene Paulo anacita, linafuula mʼcinenelo ca Cilukaoniya kuti: “Milungu yakhala ngati anthu ndipo yatsikila kwa ife!”
12 Iwo anayamba kuchula Baranaba kuti Zeu, koma Paulo anali kumuchula kuti Heme, cifukwa ndi amene anali kutsogolela polankhula.
13 Ndiyeno wansembe wa Zeu, amene kacisi wake anali pafupi ndi khomo lolowela mumzindawo, anabweletsa ngʼombe zamphongo ndi nkhata zamaluwa pa mageti. Ndipo anafuna kupeleka nsembe pamodzi ndi khamu la anthulo.
14 Koma atumwiwo, Baranaba ndi Paulo, atamva zimenezi anangʼamba zovala zawo nʼkuthamanga kukalowa mʼkhamu la anthulo akufuula kuti:
15 “Anthu inu, n’cifukwa ciyani mukucita zimenezi? Ifenso ndife anthu okhala ndi zofooka ngati inu. Ife tikulengeza uthenga wabwino kwa inu kuti muleke kucita zinthu zopandapakezi nʼkuyamba kulambila Mulungu wamoyo, amene anapanga kumwamba, dziko lapansi, nyanja ndi zonse zokhala mmenemo.
16 Mʼmibadwo ya mʼmbuyomu iye analola anthu a mitundu yonse kuti aziyenda mʼnjila zawo.
17 Ngakhale n’telo, sanangokhala wopanda umboni wakuti anacita zabwino. Anakupatsani mvula kucokela kumwamba ndi nyengo zimene zokolola zanu zimakhala zambili. Anadzazanso mitima yanu ndi cakudya komanso cimwemwe.”
18 Ngakhale kuti atumwiwo ananena zimenezi, zinavutabe kuletsa khamu la anthulo kupeleka nsembe kwa iwo.
19 Koma Ayuda obwela kucokela ku Antiokeya ndi ku Ikoniyo anakopa anthuwo. Conco iwo anaponya miyala Paulo nʼkumuguzila kunja kwa mzinda poganiza kuti wafa.
20 Koma ophunzila atamuzungulila, anauka nʼkulowa mumzinda. Tsiku lotsatila anacoka kupita ku Debe ndi Baranaba.
21 Pambuyo polengeza uthenga wabwino mumzindawu nʼkupanga ophunzila ambili ndithu, iwo anabwelela ku Lusitara, ku Ikoniyo, ndi ku Antiokeya.
22 Kumeneko iwo analimbitsa ophunzila komanso kuwathandiza kuti akhalebe m’cikhulupililo. Anali kuwauza kuti: “Tiyenela kukumana ndi masautso ambili kuti tikalowe mu Ufumu wa Mulungu.”
23 Iwo anasankhanso akulu mumpingo uliwonse, ndipo anapemphela ndi kusala kudya, kenako anawapeleka kwa Yehova Mulungu amene iwo anayamba kumukhulupilila.
24 Ndiyeno anadutsa ku Pisidiya nʼkupita ku Pamfiliya.
25 Ndipo atatsiliza kulalikila mawu a Mulungu ku Pega, anapita ku Ataliya.
26 Pocoka kumeneko anayenda ulendo wa pamadzi kubwelela ku Antiokeya. Kumeneku nʼkumene kumbuyoku abale anawasankha kuti Mulungu awaonetse cisomo nʼcolinga coti agwile nchito, imene tsopano anali ataitsiliza.
27 Iwo atafika kumeneko anasonkhanitsa anthu a mumpingo, ndipo anawafotokozela zinthu zambili zimene Mulungu anacita kudzela mwa iwo. Anawafotokozelanso kuti Mulungu anatsegula khomo kuti anthu a mitundu ina akhale okhulupilila.
28 Conco anakhala ndi ophunzilawo kwa kanthawi ndithu.