Macitidwe a Atumwi 12:1-25
12 M’masiku amenewo, mfumu Herode anayamba kuzunza anthu ena a mumpingo.
2 Iye anapha Yakobo m’bale wake wa Yohane ndi lupanga.
3 Ataona kuti zimenezo zawasangalatsa Ayuda, anamanganso Petulo. (Anacita zimenezi m’masiku a Mikate Yopanda Cofufumitsa.)
4 Anamugwila n’kumuponya m’ndende, ndipo anamupeleka m’manja mwa magulu anayi a asilikali kuti azimulonda mosinthanasinthana. Gulu lililonse linali ndi asilikali anayi. Colinga cake cinali cakuti amuzenge mlandu pamaso pa anthu pambuyo pa Pasika.
5 Conco Petulo anasungidwa m’ndendemo, koma mpingo unali kumupemphelela kwambili kwa Mulungu.
6 Herode atatsala pang’ono kumutulutsa Petulo kuti akamuzenge mlandu, Petuloyo anali gone usiku umenewo atamangidwa maunyolo awili pakati pa asilikali awili. Ndipo pakhomo panali alonda amene anali kulonda ndendeyo.
7 Koma mwadzidzidzi, mngelo wa Yehova anaimilila, ndipo m’citolokosimo munawala. Pomuutsa, mngeloyo anagunduza Petulo m’nthiti, nati: “Uka mwamsanga!” Basi maunyolo amene anam’manga nawo anagwa pansi.
8 Mngeloyo anamuuza kuti: “Vala zovala zako ndi nsapato zako.” Iye anavaladi. Pamapeto pake anamuuza kuti: “Vala covala cako cakunja ndipo uzindilondola.”
9 Iye anatuluka ndipo anapitiliza kumulondola, koma sanadziwe kuti zimene zinali kucitika kudzela mwa mngeloyo zinali zenizeni. Anaganiza kuti anali kuona masomphenya.
10 Atapitilila gulu loyamba la asilikali a pageti ndi laciwili, anafika pageti yacitsulo yotulukila popita mumzinda, ndipo inatseguka yokha. Atatuluka anayenda naye msewu umodzi, ndipo mwadzidzidzi mngeloyo anamucokela.
11 Ndiyeno Petulo atazindikila zimene zinali kucitika anati: “Tsopano ndadziwa kuti Yehova anatumiza mngelo wake kudzandipulumutsa m’manja mwa Herode, komanso ku zonse zimene Ayuda anali kuyembekezela kuti zicitike.”
12 Atazindikila zimenezi, iye anapita kunyumba ya Mariya, mayi wa Yohane wochedwanso Maliko. Kumeneko anthu ambili anasonkhana ndipo anali kupemphela.
13 Petulo atagogoda pakhomo la geti, mtsikana wanchito dzina lake Roda anabwela kuti aone amene anali kugogoda.
14 Mtsikanayo atazindikila kuti amene anali kulankhula anali Petulo, anakondwela kwambili moti sanatsegule getiyo, koma anathamangila mkati kukafotokoza kuti Petulo ali panja pageti.
15 Iwo anauza mtsikanayo kuti: “Wacita misala iwe!” Koma iye analimbikila kuwauza kuti zimene anali kukamba ndi zoona. Ndiyeno iwo anayamba kunena kuti: “Ndi mngelo wake.”
16 Koma Petulo anapitiliza kugogoda. Iwo atatsegula citseko anaona kuti ndi iyedi, ndipo anadabwa kwambili.
17 Koma iye anawauza anthuwo ndi dzanja lake kuti akhale cete, ndipo anawafotokozela mwatsatanetsatane mmene Yehova anamutulutsila m’ndende. Ndiyeno anati: “Mukauze Yakobo ndi abale ena nkhani imeneyi.” Atanena zimenezi anatuluka n’kupita kumalo ena.
18 Kutaca, asilikali anasokonezeka kwambili posadziwa zimene zacitikila Petulo.
19 Herode anafunafuna Petulo mosamala. Ndipo popeza kuti sanamupeze, anapanikiza alonda ndi mafunso n’kulamula kuti awatenge akawapatse cilango. Kenako Herode anacoka ku Yudeya nʼkupita ku Kaisareya, kumeneko anakhalako kwa kanthawi ndithu.
20 Herode anawakwiyila kwambili anthu a ku Turo ndi Sidoni. Conco iwo mogwilizana anapita kwa iye, ndipo pambuyo ponyengelela Balasito, munthu amene anali kuyang’anila zocitika za panyumba ya mfumu, anapempha mtendele. Anatelo cifukwa dziko lawo linali kudalila cakudya cocokela mʼdziko la mfumuyo.
21 Pa tsiku lina limene anasankha, Herode anavala zovala zacifumu nʼkukhala pampando woweluzila milandu, ndipo anayamba kulankhula ndi anthu.
22 Ndiyeno anthu amene anasonkhanawo anayamba kufuula kuti: “Mawu awa ndi a mulungu osati a munthu!”
23 Nthawi yomweyo mngelo wa Yehova anamukantha* cifukwa sanalemekeze Mulungu, ndipo anadyedwa ndi mphutsi n’kumwalila.
24 Koma mawu a Yehova anapitiliza kufalikila, ndipo anthu ambili anakhala okhulupilila.
25 Baranaba ndi Saulo atatsiliza nchito yopeleka thandizo ku Yerusalemu, anabwelela. Ndipo popita anatenga Yohane wochedwanso Maliko.
Mawu a m'Munsi
^ Kapena kuti, “anamudwalitsa.”