Uthenga Wabwino Wolembedwa ndi Luka 24:1-53
24 Koma pa tsiku loyamba la mlunguwo, iwo anapita m’mamawa kumandako,* atanyamula zonunkhilitsa zimene anakonza.
2 Koma anapeza kuti cimwala ca pamandawo* cakunkhunizidwila kumbali.
3 Ndipo atalowa m’mandawo sanaupeze mtembo wa Ambuye Yesu.
4 Akudabwa ndi zimenezi, anangoona kuti amuna awili ovala zovala zonyezimila aimilila pafupi nawo.
5 Azimayiwo anacita mantha, ndipo anawelamitsa nkhope zawo pansi. Ndiyeno amunawo anawafunsa kuti: “N’cifukwa ciyani mukufuna munthu wamoyo pakati pa anthu akufa?
6 Iye sali kuno, waukitsidwa. Kumbukilani zimene anakuuzani pamene anali ku Galileya.
7 Anati Mwana wa munthu ayenela kupelekedwa m’manja mwa anthu ocimwa ndi kuphedwa pamtengo, ndipo pa tsiku lacitatu adzauka.”
8 Pamenepo iwo anakumbukila mawu ake,
9 ndipo anacoka kumandako* n’kupita kukafotokoza zinthu zonsezi kwa atumwi 11 aja, komanso kwa ena onse.
10 Azimayiwo anali Mariya Mmagadala, Jowana, komanso Mariya mayi ake a Yakobo. Ndiponso azimayi ena onse amene anali nawo, anali kufotokozela atumwi zinthu zimenezi.
11 Koma zimenezi zinaoneka ngati zacabecabe kwa iwo, ndipo sanawakhulupilile azimayiwo.
12 Koma Petulo ananyamuka n’kuthamangila kumandako,* ndipo atasuzila m’mandamo anangoona nsalu zokha. Conco, anacoka ndi kupita ali wodabwa ndi zimene zinacitika.
13 Koma patsiku limenelo, awili a iwo anali kupita ku mudzi wochedwa Emau, umene unali pa mtunda wa makilomita pafupifupi 11* kucokela ku Yerusalemu.
14 Iwo anali kukambilana zinthu zonsezi zimene zinacitika.
15 Tsopano pamene anali kukambilana zinthu zimenezi, Yesu anafika n’kuyamba kuyenda nawo limodzi.
16 Koma iwo sanathe kumuzindikila.
17 Iye anawafunsa kuti: “Kodi ndi nkhani zotani zimene mukukambilana pamene mukuyenda?” Iwo anangoima cilili akuoneka acisoni.
18 Mmodzi wa iwo dzina lake Keleopa anamuyankha kuti: “Kodi iwe ukukhala wekha mu Yerusalemu monga mlendo,* ndipo sudziwa zimene zacitika mmenemo m’masiku apitawa?”
19 Iye anawafunsa kuti: “Zinthu zotani?” Iwo anamuyankha kuti: “Zinthu zokhudza Yesu Mnazareti, amene anali mneneli wamphamvu m’zocita ndi m’mawu pamaso pa Mulungu, komanso pamaso pa anthu onse.
20 Ndiponso zokhudza mmene ansembe athu aakulu ndi olamulila anamupelekela kuti aphedwe, ndi kumukhomelela pamtengo.
21 Koma ife, tinali kuyembekezela kuti munthu uyu ndiye adzapulumutsa Aisiraeli. Inde, ndipo kuwonjezela apo, lelo ndi tsiku lacitatu kucokela pamene zinthuzi zinacitika.
22 Komanso azimayi ena m’gulu lathu atidabwitsa kwambili, cifukwa anapita ku manda* m’mamawa kwambili.
23 Ndipo ataona kuti mtembo wake mulibe m’mandamo, abwelako n’kutifotokozela kuti aona masomphenya a angelo amene awauza kuti Yesu ali moyo.
24 Ndiyeno ena pakati pathu anapita kumandako, ndipo apeza kuti m’mandamo mulibe aliyense mogwilizana ndi zimene azimayiwo anena. Koma iwo sanamuone.”
25 Conco iye anawauza kuti: “Opanda nzelu inu komanso ocedwa* kukhulupilila zonse zimene aneneli ananena!
26 Kodi sikunali koyenela kuti Khristu avutike ndi zinthu zonsezi n’kulowa mu ulemelelo wake?”
27 Ndiyeno anayamba kuwafotokozela zinthu zonse zokhudza iye m’Malemba onse kuyambila zolemba za Mose, komanso za aneneli onse.
28 Ndiyeno iwo anayandikila mudzi umene anali kupitako, ndipo iye anacita monga akufuna kupitilila mudziwo.
29 Koma iwo anamucondelela kuti akhalebe nawo. Anati: “Khalanibe nafe cifukwa kwayamba kuda, ndiponso tsiku latsala pang’ono kutha.” Iye atamva zimenezo analowa m’nyumba n’kukhala nawo.
30 Pamene anali kudya nawo cakudya, anatenga mkate n’kuudalitsa, kenako anaunyemanyema n’kuyamba kuwapatsa.
31 Pamenepo maso awo anatseguka ndipo anamuzindikila, koma Yesu anangozimililika pakati pawo.
32 Iwo anayamba kukambilana kuti: “Kodi si paja mawu ake anatikhudza kwambili mumtima, pamene anali kulankhula nafe mumsewu muja, ndi kutifotokozela Malemba momveka bwino?”
33 Pa ola lomwelo iwo ananyamuka n’kubwelela ku Yerusalemu, ndipo anapeza atumwi 11 aja ndi anthu ena amene anasonkhana nawo pamodzi.
34 Iwo anati: “Kukamba zoona, Ambuye anaukitsidwa kwa akufa, ndipo anaonekela kwa Simoni!”
35 Ndiyeno anafotokoza zimene zinacitika pamsewu komanso mmene anamudziwila pamene ananyemanyema mkate.
36 Ali mkati mokamba zimenezi, Yesu anaimilila pakati pawo ndi kuwauza kuti: “Mtendele ukhale nanu.”
37 Koma cifukwa cakuti iwo anadzidzimuka ndi kucita mantha, anaganiza kuti akuona mzimu.
38 Cotelo iye anawafunsa kuti: “N’cifukwa ciyani mukuvutika mumtima komanso kukayikila m’mitima yanu?
39 Onani manja ndi mapazi anga kuti mutsimikize kuti ndine. Ndikhudzeni muone, cifukwa mzimu ulibe mnofu ndi mafupa, koma ine monga mukuonela ndili nazo.”
40 Pokamba zimenezi, anawaonetsa manja ndi mapazi ake.
41 Koma popeza iwo sanakhulupililebe cifukwa ca cimwemwe ndi kudabwa, iye anawafunsa kuti: “Kodi muli ndi cakudya ciliconse?”
42 Conco iwo anamupatsa cidutswa ca nsomba yowocha,
43 ndipo anacitenga n’kudya iwo akuona.
44 Kenako anawauza kuti: “Awa ndi mawu amene ndinakuuzani ndikali nanu akuti, zinthu zonse zokhudza ine zimene zinalembedwa m’Cilamulo ca Mose, m’zolemba za Aneneli, komanso zolembedwa mu Masalimo ziyenela kukwanilitsidwa.”
45 Kenako anatsegulilatu maganizo awo kuti amvetsetse tanthauzo la Malemba.
46 Ndipo anawauza kuti: “Malemba amati Khristu adzavutika, ndipo pa tsiku lacitatu adzauka kwa akufa.
47 Ndipo m’dzina lake, uthenga wakuti anthu afunika kulapa macimo awo kuti akhululukidwe, udzalalikidwa ku mitundu yonse, kuyambila ku Yerusalemu.
48 Inuyo mudzakhala mboni za zinthu zimenezi.
49 Ndipo taonani, ndidzakutumizilani cimene Atate wanga anakulonjezani. Koma inu mukhalebe mumzindawu, kufikila mutalandila mphamvu yocokela kumwamba.”
50 Ndiyeno anawatsogolela mpaka kukafika nawo ku Betaniya, ndipo kumeneko anakweza manja ake n’kuwadalitsa.
51 Pamene anali kuwadalitsa anawasiya, ndipo Mulungu anamutenga ndi kupita naye kumwamba.
52 Ndiyeno anamugwadila* n’kubwelela ku Yerusalemu ali osangalala kwambili.
53 Nthawi zonse iwo anali kukhala m’kacisi kutamanda Mulungu.
Mawu a m'Munsi
^ Kapena kuti, “manda acikumbutso.”
^ Kapena kuti, “manda acikumbutso.”
^ Kapena kuti, “manda acikumbutso.”
^ Kapena kuti, “manda acikumbutso.”
^ M’cinenelo coyambila, “masitadiya 60. Sitadiya imodzi inali kukwana mamita 185.”
^ Ma Baibulo ena amati, “Kodi ndiwe mlendo yekhayo mu Yerusalemu amene sukudziŵa?”
^ Kapena kuti, “manda acikumbutso.”
^ Kapena kuti, “amtima wocedwa.”
^ Kapena kuti, “anamuwelamila.”