Uthenga Wabwino Wolembedwa ndi Luka 22:1-71

  • Ansembe akonza ciwembu ca kupha Yesu (1-6)

  • Kukonzekela Pasika wothela (7-13)

  • Kukhazikitsidwa kwa Mgonelo wa Ambuye (14-20)

  • “Wondipeleka uja ali nane pathebulo pano” (21-23)

  • Akangana kwambili zakuti wamkulu ndani (24-27)

  • Cipangano ca Yesu ca Ufumu (28-30)

  • Yesu akambilatu zakuti Petulo adzamukana (31-34)

  • Kufunika kokhala okonzeka; malupanga awili (35-38)

  • Pemphelo la Yesu pa Phili la Maolivi (39-46)

  • Yesu agwidwa (47-53)

  • Petulo akana Yesu (54-62)

  • Yesu acitidwa zacipongwe (63-65)

  • Azengedwa mlandu ku Khoti Yaikulu ya Ayuda (66-71)

22  Tsopano Cikondwelelo ca Mikate Yopanda Zofufumitsa cimenenso cimachedwa Pasika, cinali citayandikila. 2  Ndiyeno ansembe aakulu ndi alembi anali kufunafuna njila yabwino yomuphela Yesu, cifukwa anali kuopa anthu. 3  Kenako Satana analowa mwa Yudasi wochedwa Isikariyoti, amene anali mmodzi wa atumwi 12 aja. 4  Ndipo anapita kukakambilana ndi ansembe aakulu komanso akapitawo a pakacisi za mmene angamupelekele kwa iwo. 5  Iwo anakondwela ndi zimenezi, ndipo anagwilizana kuti amupatse ndalama zasiliva. 6  Cotelo iye anavomela, ndipo anayamba kufunafuna mpata wabwino woti amupeleke kwa iwo popanda khamu la anthu pafupi. 7  Tsopano tsiku la Cikondwelelo ca Mikate Yopanda Zofufumitsa linafika, tsiku limene nsembe ya Pasika inali kuyenela kupelekedwa. 8  Conco Yesu anatuma Petulo ndi Yohane n’kuwauza kuti: “Pitani mukakonze Pasika kuti tidye.” 9  Iwo anamufunsa kuti: “Mufuna tikakonzele kuti?” 10  Iye anawauza kuti: “Mukakalowa mumzinda, mwamuna wonyamula mtsuko wa madzi adzakumana nanu. Mukamutsatile m’nyumba imene akalowe. 11  Ndipo mukauze mwininyumbayo kuti, ‘Mphunzitsi akuti kwa inu: “Kodi cipinda ca alendo cili kuti, cimene ndingadyelemo Pasika pamodzi ndi ophunzila anga?”’ 12  Munthuyo adzakuonetsani cipinda cacikulu cam’mwamba cokonzedwa bwino. Mukakonzele mmenemo.” 13  Conco ophunzilawo anapita, ndipo zinacitikadi mmene Yesu anawauzila. Iwo anakonza zonse zofunikila za Pasika. 14  Cotelo nthawi itakwana, iye anakhala pa thebulo pamodzi ndi atumwi. 15  Kenako anawauza kuti: “Ndakhala ndikulakalaka kwambili kudya Pasika uyu pamodzi nanu ndisanayambe kuzunzika. 16  Pakuti ndikukuuzani, sindidzadyanso Pasika uyu kufikila colinga cake citakwanilitsidwa mu Ufumu wa Mulungu.” 17  Ndiyeno atalandila kapu, anayamika n’kunena kuti: “Aneni, ndipo imwani mopatsilana. 18  Pakuti ndikukuuzani kuti, kuyambila tsopano, sindidzamwanso cakumwa cocokela ku mphesa kufikila Ufumu wa Mulungu utabwela.” 19  Komanso, anatenga mtanda wa mkate n’kuyamika, ndipo anaunyemanyema n’kuupeleka kwa iwo. Kenako anati: “Mkate uwu ukuimila thupi langa limene lidzapelekedwa kaamba ka inu. Muzicita zimenezi pondikumbukila.” 20  Anacitanso cimodzimodzi ndi kapu pambuyo pa cakudya ca madzulo. Iye anati: “Kapu iyi ikuimila cipangano catsopano pa maziko a magazi anga amene akhetsedwe kaamba ka inu. 21  “Koma taonani! Wondipeleka uja ali nane pathebulo pano. 22  Pakuti ndithudi, Mwana wa munthu akupita mogwilizana ndi zimene zinanenedwelatu. Koma tsoka kwa munthu amene akumupeleka!” 23  Conco iwo anayamba kukambilana zakuti ndani pakati pawo amene afuna kucita zimenezi. 24  Komanso, iwo anayamba kukangana kwambili zakuti ndani pakati pawo amene anali kuonedwa kuti ndi wamkulu kwambili. 25  Koma iye anawauza kuti: “Mafumu a mitundu ina amapondeleza anthu awo, ndipo amene ali ndi ulamulilo pa anthu, amadziwika kuti ndi anthu amene amacitila ena zabwino. 26  Inu musakhale otelo. Koma wamkulu kwambili pakati panu, akhale ngati wamng’ono kwambili, komanso amene akutsogolela akhale ngati wotumikila. 27  Kodi wamkulu ndani, amene akudya pathebulo kapena amene akutumikila? Kodi si uja amene akudya pathebulo? Koma ine ndili pakati panu monga wotumikila. 28  “Inu mwakhalabe nane m’mayeselo anga. 29  Ndipo ine ndikucita nanu cipangano, monga mmene Atate wanga anacitila cipangano ca ufumu ndi ine, 30  kuti mukadye ndi kumwa pathebulo mu Ufumu wanga, komanso kuti mukakhale pa mipando yacifumu n’kuweluza mafuko 12 a Isiraeli. 31  “Simoni, Simoni, taona! Satana akufuna kuti akupepeteni nonsenu monga tiligu. 32  Koma ine ndakupemphelela mocondelela kuti cikhulupililo cako cisathe. Conco ukabwelela, ukalimbikitse abale ako.” 33  Kenako iye anauza Yesu kuti: “Ambuye, ndine wokonzeka kupita nanu kundende komanso kufa nanu.” 34  Koma iye anati: “Ndikukuuza Petulo, tambala asanalile lelo, iwe undikana katatu kuti sundidziwa.” 35  Iye anawauzanso kuti: “Pamene ndinakutumani popanda kunyamula cikwama ca ndalama, cola ca zakudya, komanso nsapato, simunasowe kalikonse, si conco?” Iwo anayankha kuti: “Inde!” 36  Ndiyeno anawauza kuti: “Koma tsopano amene ali ndi cikwama ca ndalama acitenge, atengenso cola ca zakudya, ndipo amene alibe lupanga, agulitse covala cake cakunja n’kugula lupanga. 37  Pakuti ndikukuuzani kuti zimene zinalembedwa ziyenela kukwanilitsidwa mwa ine, zakuti, ‘Anaikidwa pa gulu la anthu osamvela malamulo.’ Cifukwa izi zikukwanilitsidwa pa ine.” 38  Ndiyeno iwo anati: “Ambuye, onani! Tili ndi malupanga awili.” Iye anawauza kuti: “Amenewa ndi okwanila.” 39  Atacoka kumeneko, iye mwacizolowezi cake anapita ku Phili la Maolivi, ndipo ophunzila ake nawonso anamutsatila. 40  Atafika kumeneko anawauza kuti: “Pitilizani kupemphela kuti musalowe m’mayeselo.” 41  Ndipo iye anacoka pamene panali ophunzilawo, n’kupita capatali, ngati pomwe mwala ungagwele munthu atauponya. Kumeneko anagwada pansi n’kuyamba kupemphela, 42  kuti: “Atate, ngati mufuna, ndicotseleni kapu iyi. Koma lolani kuti cifunilo canu cicitike, osati canga.” 43  Kenako, mngelo wocokela kumwamba anaonekela kwa iye, ndipo anamulimbikitsa. 44  Koma iye anavutika kwambili mumtima, moti anapitiliza kupemphela mocokela pansi pa mtima, ndipo thukuta lake linayamba kuoneka ngati madontho a magazi amene akugwela pansi. 45  Atatsiliza kupemphela, ananyamuka n’kupita pamene panali ophunzila ake, ndipo anawapeza akugona, atafooka ndi cisoni. 46  Iye anawafunsa kuti: “N’cifukwa ciyani mukugona? Ukani, ndipo pitilizani kupemphela kuti musalowe m’mayeselo.” 47  Ali mkati molankhula, kunabwela khamu la anthu. Anthuwo anali ndi munthu wochedwa Yudasi, mmodzi wa atumwi 12 aja, ndipo iye ndiye anali kuwatsogolela. Ndiyeno Yudasi anapita pamene panali Yesu kuti amupsompsone. 48  Koma Yesu anamufunsa kuti: “Yudasi, ukupeleka Mwana wa munthu mwa kumupsompsona?” 49  Amene anali pafupi ndi Yesu ataona zimene zinali kucitika, anati: “Ambuye, kodi tiwateme ndi lupanga?” 50  Mmodzi wa iwo anatemadi kapolo wa mkulu wa ansembe, mpaka kumudula khutu la kudzanja lamanja. 51  Koma Yesu anayankha kuti: “Musacite zimenezi.” Kenako anagwila khutu lija n’kumucilitsa. 52  Ndiyeno Yesu anafunsa ansembe aakulu, akapitawo a pakacisi komanso akulu amene anabwela kudzamugwila kuti: “N’cifukwa ciyani mwabwela mutanyamula malupanga ndi nkholi ngati kuti mukubwela kudzagwila wacifwamba? 53  Pamene ndinali kukhala nanu m’kacisi tsiku lililonse simunandigwile. Koma ino ndi nthawi yanu komanso ya ulamulilo wa anthu amene ali mumdima.” 54  Ndiyeno anamugwila n’kupita naye. Kenako anamupeleka m’nyumba ya mkulu wa ansembe, koma Petulo anali kuwatsatila capatali. 55  Iwo anayatsa moto mkati mwa bwalo ndipo onse anakhala pansi. Nayenso Petulo anakhala pansi pakati pawo. 56  Koma mtsikana wina wanchito atamuona atakhala pafupi ndi moto wowala, anamuyang’anitsitsa n’kunena kuti: “Awanso anali naye limodzi.” 57  Koma iye anakana kuti: “Mtsikana iwe, munthu ameneyo ine sindimudziwa.” 58  Patapita kanthawi kocepa, munthu wina anamuona ndipo anati: “Inunso ndinu mmodzi wa iwo.” Koma Petulo anati: “Mwamuna iwe, sindine ayi.” 59  Ndiyeno patapita pafupifupi ola limodzi, munthu winanso anayamba kukamba motsimikiza kuti: “Mosakayikila, munthu ameneyu analinso naye limodzi, cifukwa ndi Mgalileya!” 60  Koma Petulo anati: “Mwamuna iwe, zimene ukamba ine sindizidziwa.” Nthawi yomweyo, ali mkati molankhula tambala analila. 61  Pamenepo Ambuye anaceuka ndi kuyang’ana Petulo, ndipo Petulo anakumbukila mawu amene Ambuye anamuuza akuti: “Tambala asanalile lelo, iwe undikana katatu.” 62  Pamenepo anatuluka panja n’kuyamba kulila mwacisoni kwambili. 63  Ndiyeno anthu amene anagwila Yesu aja, anayamba kumucita zacipongwe ndi kumumenya. 64  Kenako iwo anamuphimba kumaso n’kumamufunsa kuti: “Lotela! Wakumenya ndani?” 65  Iwo anakamba zinthu zina zambili zomunyoza. 66  Ndiyeno kutaca, bungwe la akulu la anthu, pamodzi ndi ansembe aakulu komanso alembi, anasonkhana pamodzi, ndipo anapita naye mu holo yawo ya Khoti Yaikulu ya Ayuda* n’kunena kuti: 67  “Tiuze ngati ndiwe Khristu.” Koma iye anawauza kuti: “Ngakhale n’takuuzani, simungakhulupilile ayi. 68  Komanso ndikakufunsani funso, simungandiyankhe. 69  Koma kuyambila tsopano mpaka m’tsogolo, Mwana wa munthu adzakhala kudzanja lamanja lamphamvu la Mulungu.” 70  Atamva zimenezi, onse anati: “Ndiye kodi ndiwe Mwana wa Mulungu?” Iye anawayankha kuti: “Inuyo mwanena nokha kuti ndine Mwana wa Mulungu.” 71  Iwo anati: “Kodi n’kufunilanji umboni wina? Cifukwa apa tadzimvela tokha kucokela pakamwa pake.”

Mawu a m'Munsi

M’cinenelo coyambilila, “Sanihedirini.”