Uthenga Wabwino Wolembedwa ndi Luka 11:1-54
11 Tsopano Yesu anali kupemphela pa malo enaake, ndipo atatsiliza, mmodzi wa ophunzila ake anamuuza kuti: “Ambuye, tiphunzitseni mopemphelela monga mmene Yohane anaphunzitsila ophunzila ake.”
2 Pamenepo anawauza kuti: “Nthawi zonse mukamapemphela, muzinena kuti: ‘Atate, dzina lanu liyeletsedwe.* Ufumu wanu ubwele.
3 Mutipatse cakudya ca tsiku lililonse malinga ndi zofunikila zathu pa tsikulo.
4 Ndipo mutikhululukile macimo athu, cifukwa nafenso timakhululukila aliyense amene watilakwila,* ndiponso mutithandize kuti tisagonje tikamayesedwa.’”
5 Kenako anawauza kuti: “Tiyelekeze kuti mmodzi wa inu ali ndi mnzake, ndipo iye wapita kwa mnzakeyo pakati pa usiku n’kumuuza kuti, ‘Mnzangawe, ndibwelekeko mitanda itatu ya mkate,
6 cifukwa mnzanga wina wangofika kumene kucokela ku ulendo, ndipo ndilibe ciliconse comupatsa.’
7 Koma mnzakeyo akuyankha ali m’nyumba kuti: ‘Usandivutitse, citseko takhoma kale. Ndipo ine ndi ana anga tagona kale. Sindingauke kuti ndikupatse kanthu.’
8 Ndithu ndikukuuzani, munthuyo adzaukabe ndi kum’patsa ciliconse cimene akufuna, osati cifukwa cakuti ndi bwenzi lake, koma cifukwa ca kulimbikila kwake.
9 Conco ndikukuuzani kuti, pemphanibe, ndipo adzakupatsani. Pitilizani kufunafuna, ndipo mudzapeza. Gogodanibe ndipo adzakutsegulilani.
10 Pakuti aliyense wopempha amalandila, ndipo aliyense wofunafuna amapeza, ndiponso aliyense wogogoda adzamutsegulila.
11 Ndithudi, kodi pali tate pakati panu amene mwana wake akam’pempha nsomba angamupatse njoka m’malo mwa nsomba?
12 Kapenanso ngati angamupemphe dzila, kodi angamupatse cinkhanila?
13 Cotelo ngati inu, ngakhale kuti ndinu oipa, mumadziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, kuli bwanji Atate wanu wakumwamba? Ndithudi, iye adzapeleka mzimu woyela kwa amene amamupempha.”
14 Zitatha izi, Yesu anatulutsa ciwanda mwa munthu winawake comwe cinali kumulepheletsa kulankhula. Ciwandaco citatuluka, munthu wosalankhulayo anayamba kulankhula, ndipo khamu la anthu linadabwa kwambili.
15 Koma ena a iwo anati: “Ameneyu amatulutsa ziwanda ndi mphamvu za Belezebule,* wolamulila ziwanda.”
16 Koma ena pofuna kumuyesa, anayamba kumukakamiza kuti awaonetse cizindikilo cocokela kumwamba.
17 Yesu atadziwa maganizo awo anawauza kuti: “Ufumu uliwonse wogawikana umatha, ndipo nyumba iliyonse yogawikana imagwa.
18 Mofanana ndi zimenezi, ngati Satana nayenso ndi wogawikana, kodi ufumu wake ungakhalepo bwanji? Pakuti inu mukunena kuti ndimatulutsa ziwanda ndi mphamvu za Belezebule.
19 Ngati ine ndimatulutsa ziwanda ndi mphamvu za Belezebule, nanga ophunzila anu amazitulutsa ndi mphamvu za ndani? Ndiye cifukwa cake iwo adzakuweluzani.
20 Koma ngati ndimatulutsa ziwanda ndi cala ca Mulungu, ndiye kuti Ufumu wa Mulungu wakufikanidi modzidzimutsa.
21 Munthu wamphamvu amene ali ndi zida zokwanila akamalonda nyumba yake, katundu wake umakhala wotetezeka.
22 Koma munthu wina wamphamvu kuposa iye akabwela n’kumugonjetsa, amamulanda zida zake zonse zimene anali kudalila, ndipo amagawila anthu ena katundu amene walandayo.
23 Aliyense amene sali kumbali yanga akutsutsana nane, ndipo aliyense amene sakundithandiza kusonkhanitsa anthu kwa ine akuwamwaza.
24 “Mzimu wonyansa ukatuluka mwa munthu, umadutsa m’malo opanda madzi kufunafuna popumulila. Koma ngati sunapeze malo alionse, umati, ‘Ndibwelela kunyumba yanga imene ndinatulukamo.’
25 Ndipo ukafika, umapeza kuti m’nyumbamo ndi mopsela komanso mokonza bwino.
26 Kenako umapita n’kukatenga mizimu ina 7 yoipa kwambili kuposa umenewo, ndipo yonse imadzalowa m’nyumbamo n’kumakhala mmenemo. Pamapeto pake munthuyo amakhala woipa kwambili kuposa poyamba.”
27 Ali mkati mokamba zimenezi, mayi wina pagulu la anthu limenelo anafuula kwa iye kuti: “Wacimwemwe ndi mayi amene anakubelekani, amenenso munayamwa mawele ake!”
28 Koma iye anati: “Ayi, m’malo mwake, acimwemwe ndi anthu amene akumva mawu a Mulungu ndi kuwasunga!”
29 Pamene khamu la anthu linali kuculukilaculukila, iye anayamba kunena kuti: “M’badwo uwu ndi woipa. Ukufuna cizindikilo, koma sudzapatsidwa cizindikilo ciliconse kupatulapo cizindikilo ca Yona.
30 Monga mmene Yona anakhalila cizindikilo kwa anthu a ku Nineve, Mwana wa munthu nayenso adzakhala cizindikilo ku m’badwo uwu.
31 Mfumukazi ya kum’mwela idzaukitsidwa pa Tsiku la Ciweluzo pamodzi ndi anthu a m’badwo uwu ndipo idzawatsutsa, cifukwa inacokela ku malekezelo a dziko lapansi n’kubwela kuti idzamve nzelu za Solomo. Koma onani! winawake woposa Solomo ali pano.
32 Anthu a ku Nineve adzauka pa Tsiku la Ciweluzo pamodzi ndi m’badwo uwu, ndipo adzautsutsa cifukwa analapa atamva ulaliki wa Yona. Koma onani! winawake woposa Yona ali pano.
33 Munthu akayatsa nyale, saiika pa malo obisika kapena kuibwinikila ndi thadza,* koma amaiika pa coikapo nyale kuti olowa m’nyumbamo aziona kuwala.
34 Nyale ya thupi ndi diso lako. Diso lako likalunjika pa cinthu cimodzi,* thupi lako lonse limakhala lowala. Koma ngati ndi ladyela,* nalonso thupi lako limacita mdima.
35 Conco khala maso kuti kuwala kumene kuli mwa iwe kusakhale mdima.
36 Cotelo ngati thupi lako lonse n’lowala, ndipo palibe mbali imene ili ndi mdima, thupi lako lonse lidzakhala lowala mmene nyale imawalila pokuunikila.”
37 Yesu atatsiliza kulankhula izi, Mfarisi wina anamupempha kuti akadye naye cakudya. Conco anakalowa m’nyumba yake ndipo anakhala pathebulo n’kuyamba kudya naye.
38 Koma Mfarisiyo anadabwa ataona kuti Yesu akudya cakudya cosasamba m’manja.*
39 Cotelo Ambuye anamuuza kuti: “Inu Afarisi mumayeletsa kunja kwa kapu ndi mbale, koma mumtima mwanu ndi modzala dyela komanso zinthu zoipa.
40 Anthu opusa inu! Kodi amene anapanga kunja si amenenso anapanga mkati?
41 Koma mphatso zacifundo* zimene mumapeleka zizicokela mu mtima. Ndipo onani! zonse zokhudza inu zidzakhala zoyela.
42 Koma tsoka kwa inu Afarisi, cifukwa mumapeleka cakhumi ca minti ndi luwe, komanso ca mbewu zilizonse zakudimba,* koma mumanyalanyaza cilungamo ndi cikondi ca Mulungu. Unali udindo wanu kucita zinthu zimenezi, koma simunafunike kunyalanyaza zinthu zinazo.
43 Tsoka kwa inu Afarisi, cifukwa mumakonda kukhala pa mipando ya kutsogolo* m’masunagoge, ndiponso mumakonda kupatsidwa moni m’misika!
44 Tsoka kwa inu, cifukwa muli ngati manda* aja amene sakuoneka bwinobwino,* ndipo anthu amayenda pa mandawo koma osadziwa!”
45 Poyankha, mmodzi wa odziwa Cilamulo anamuuza kuti: “Mphunzitsi, pamene mwakamba izi, ndiye kuti nafenso mwatinyoza.”
46 Kenako Yesu anati: “Tsoka kwa inunso odziwa Cilamulo, cifukwa mumanyamulitsa anthu katundu wovuta kunyamula, koma inuyo simuyesa kuukhudza ngakhale ndi cala canu cokha!
47 “Tsoka kwa inu, cifukwa mumamanga manda* a aneneli koma makolo anu ndiwo anawapha!
48 Mosakayikila, inu ndinu mboni pa zimene makolo anu anacita, ndipo mukugwilizana nazo, cifukwa iwo anapha aneneliwo koma inu mukumanga manda awo.
49 Ndiye cifukwa cake nzelu ya Mulungu inanenanso kuti: ‘Ndidzawatumizila aneneli ndi atumwi, ndipo iwo adzapha ena a iwo ndi kuwazunza.
50 Adzacita izi kuti mlandu wa magazi onse amene akhetsedwa a aneneli, kuyambila pa ciyambi ca dziko, ukhale pa m’badwo uwu.*
51 Kuyambila magazi a Abele mpaka magazi a Zekariya yemwe anaphedwa pakati pa guwa la nsembe ndi kacisi.’* Ndithu ndikukuuzani, mlandu wa magazi amenewo udzakhala pa m’badwo uwu.*
52 “Tsoka kwa inu odziwa Cilamulo, cifukwa munalanda anthu kiyi yodziwila zinthu. Inuyo simunalowemo, ndipo mukutsekeleza anthu ofuna kulowamo!”*
53 Conco atacoka kumeneko, alembi ndi Afarisi anayamba kumupanikiza koopsa ndi kumuthila mafunso ena ambili,
54 ndipo anamuchela msampha kuti amukole pa zimene angakambe.
Mawu a m'Munsi
^ Kapena kuti, “likhale lopatulika; lionedwe kukhala loyela.”
^ M’cinenelo coyambilila, “ali nafe nkhongole.”
^ Dzina lina la Satana.
^ Kapena kuti, “thadza lopimila.”
^ Kapena kuti, “limaona bwino.”
^ M’cinenelo coyambilila, “loipa.”
^ Kutanthauza kusamba m’manja motsatila mwambo.
^ Kapena kuti, “mphatso kwa osauka.” Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Kapena kuti, “ndiwo zilizonse za ku dimba.”
^ Kapena kuti, “yabwino kwambili.”
^ Kapena kuti, “manda acikumbutso.”
^ Kapena kuti, “manda aja osaikidwa cizindikilo.”
^ Kapena kuti, “manda acikumbutso.”
^ Kapena kuti, “adzafunidwa kucokela ku m’badwo uwu.”
^ M’cinenelo coyambilila, “nyumba.”
^ Kapena kuti, “magazi amenewo adzafunidwa ku mbadwo uwu.”
^ Kutanthauza mu Ufumu wa kumwamba. Onani Mateyo 23:13.