Uthenga Wabwino Wolembedwa ndi Luka 1:1-80
-
Kalata yopita kwa Teofilo (1-4)
-
Mngelo Gabirieli anenelatu za kubadwa kwa Yohane M’batizi (5-25)
-
Mngelo Gabirieli anenelatu za kubadwa kwa Yesu (26-38)
-
Mariya apita kwa Elizabeti (39-45)
-
Mariya alemekeza Yehova (46-56)
-
Kubadwa kwa Yohane ndi mmene anamupatsila dzina (57-66)
-
Ulosi wa Zekariya (67-80)
1 Anthu ambili analemba nkhani yofotokoza zinthu zonse zimene zinacitika, zomwe ifenso timazikhulupilila.*
2 Enanso amene kucokela paciyambi anali mboni zoona ndi maso, komanso alengezi a uthenga wa Mulungu anatiuza zinthu zimenezi.
3 Conco inu wolemekezeka koposa, a Teofilo, ine ndasanthula zinthu zonsezi molondola kucokela paciyambi, ndipo inenso ndatsimikiza mtima kukulembelani zinthu zimenezi mwatsatanetsatane.
4 Ndacita izi kuti mutsimikize kuti zinthu zimene anakuphunzitsani ndi mawu apakamwa n’zoona.
5 M’masiku a Herode, mfumu ya Yudeya, kunali wansembe wina dzina lake Zekariya wa m’gulu la ansembe la Abiya. Mkazi wake anali wocokela mwa ana aakazi a Aroni, ndipo dzina lake anali Elizabeti.
6 Onse awili anali olungama pamaso pa Mulungu. Ndipo anali kutsatila mokhulupilika malamulo onse a Yehova.
7 Komatu analibe mwana, cifukwa Elizabeti anali wosabeleka, ndipo onse awili anali okalamba.
8 Tsopano inali nthawi yakuti gulu lake litumikile pa kacisi. Ndipo iye anali kutumikila monga wansembe pamaso pa Mulungu.
9 Mwa cizolowezi ca ansembe,* inali nthawi yake yakuti alowe m’nyumba yopatulika ya Yehova kuti akapeleke nsembe zofukiza.
10 Gulu lonse la anthu linali kupemphela panja panthawi yopeleka nsembe zofukiza.
11 Ndiyeno mngelo wa Yehova anaonekela kwa iye ataimilila ku lamanja kwa guwa lansembe zofukiza.
12 Zekariya anavutika maganizo ndi zimene anaonazo, ndipo anacita mantha kwambili.
13 Koma mngeloyo anamuuza kuti: “Usacite mantha Zekariya, cifukwa pemphelo lako locondelela lamveka, mkazi wako Elizabeti adzakubelekela mwana wamwamuna, ndipo udzamupatse dzina lakuti Yohane.
14 Iwe udzasangalala ndi kukondwela kwambili, ndipo ambili adzakondwela ndi kubadwa kwake,
15 cifukwa iye adzakhala wamkulu pamaso pa Yehova. Koma asadzamwe vinyo kapena cakumwa ciliconse coledzeletsa ngakhale pang’ono, ndipo iye adzadzazidwa ndi mzimu woyela ngakhale asanabadwe.*
16 Iye adzabwezeletsa ana ambili a Isiraeli kwa Yehova Mulungu wawo.
17 Komanso Mulungu adzamutumiza patsogolo pake ali ndi mzimu ndiponso mphamvu monga za Eliya. Adzamutumiza kuti akatembenuze mitima ya atate kuti ikhale ngati ya ana,* komanso kuti akathandize anthu osamvela kukhala ndi nzelu za anthu olungama, n’colinga cakuti akonzekeletse anthu kutumikila Yehova.”
18 Zekariya anafunsa mngeloyo kuti: “Kodi ndingatsimikize bwanji zimenezi? Cifukwa ndine wokalamba, ndipo mkazi wanga nayenso ndi wokalamba.”
19 Mngeloyo anamuyankha kuti: “Ine ndine Gabirieli, ndimaimilila pafupi ndi Mulungu, ndipo ndatumidwa kuti ndidzalankhule nawe komanso kuti ndidzalengeze uthenga wabwino umenewu kwa iwe.
20 Koma tamvela! Udzakhala cete ndipo sudzatha kulankhula mpaka tsiku limene zinthu zimenezi zidzacitike, cifukwa sunakhulupilile mawu anga amene adzakwanilitsidwa pa nthawi yake yoikika.”
21 Pa nthawiyi, anthu anali kungomuyembekezela Zekariya, ndipo iwo anadabwa kuti watenga nthawi yaitali kwambili m’nyumba yopatulikayo.
22 Atatuluka, iye sanathe kulankhula nawo. Ndipo iwo anazindikila kuti waona masomphenya m’nyumba yopatulikayo. Iye anali kungolankhula nawo ndi manja cifukwa sanali kukwanitsa kutulutsa mawu.
23 Masiku ake a utumiki* wopatulika atatha, iye anabwelela kunyumba kwake.
24 Patapita masiku angapo, mkazi wake Elizabeti anakhala ndi pathupi. Ndipo anakhala kwayekha miyezi isanu. Iye anati:
25 “Izi n’zimene Yehova wandicitila masiku ano. Iye wandikumbukila n’kucotsa kunyozeka kwanga pakati pa anthu.”
26 Elizabeti ali woyembekezela kwa miyezi 6, Mulungu anatuma mngelo Gabirieli ku mzinda wa Galileya wochedwa Nazareti.
27 Anam’tumiza kwa namwali amene Yosefe wa m’nyumba ya Davide anamulonjeza* kuti adzamukwatila. Ndipo namwaliyo dzina lake anali Mariya.
28 Mngeloyo ataonekela kwa iye, anamuuza kuti: “Moni, iwe munthu wodalitsika kwambili. Yehova ali nawe.”
29 Koma iye anadabwa kwambili ndi mawu a mngeloyo, ndipo anayamba kuganizila tanthauzo la moni umenewo.
30 Conco mngeloyo anamuuza kuti: “Usacite mantha Mariya, cifukwa Mulungu wakukomela mtima.
31 Tamvela! Udzakhala ndi pathupi, ndipo udzabeleka mwana wamwamuna. Mwanayo udzamupatse dzina lakuti Yesu.
32 Ameneyo adzakhala wamkulu ndipo adzachedwa Mwana wa Wapamwambamwamba. Yehova Mulungu adzamupatsa mpando wacifumu wa Davide atate wake.
33 Iye adzalamulila monga Mfumu panyumba ya Yakobo kwamuyaya, ndipo Ufumu wake sudzatha.”
34 Koma Mariya anafunsa mngeloyo kuti: “Nanga zimenezi zidzatheka bwanji popeza sindinagonepo ndi mwamuna?”
35 Mngeloyo anamuyankha kuti: “Mzimu woyela udzafika pa iwe, ndipo mphamvu ya Wapamwambamwamba idzakuphimba. Pa cifukwa cimeneci, amene adzabadweyo adzachedwa woyela, Mwana wa Mulungu.
36 Ndipotu tamvela! Elizabeti m’bale wako, amene anthu amamucha mayi wosabeleka, nayenso ali ndi pathupi pa mwana wamwamuna ku ukalamba wake, ndipo mwezi uno tsopano ndi wa 6.
37 Pakuti zilizonse zimene Mulungu wakamba zimatheka.”*
38 Ndiyeno Mariya anati: “Ndine pano kapolo wa Yehova. Zicitike kwa ine monga mwanenela.” Zitatelo, mngeloyo anacoka pamaso pake.
39 Conco m’masiku amenewo, Mariya ananyamuka mwamsanga kupita ku dziko la mapili, ku mzinda wa m’dela la fuko la Yuda.
40 Ndipo analowa m’nyumba ya Zekariya n’kupeleka moni kwa Elizabeti.
41 Tsopano Elizabeti atamva moni wa Mariya, mwana amene anali m’mimba mwake analumpha, ndipo Elizabetiyo anadzazidwa ndi mzimu woyela.
42 Ndiyeno, iye analankhula mokweza mawu kuti: “Ndiwe wodalitsika kuposa akazi onse, ndipo mwana amene udzabeleke, nayenso ndi wodalitsika!
43 Ndine ndani ine kuti mayi wa Ambuye wanga abwele kudzandiona?
44 Cifukwa n’tamva moni wako, mwana amene ali m’mimba mwangamu walumpha ndi cisangalalo.
45 Komanso ndiwe wacimwemwe pakuti unakhulupilila, cifukwa Yehova adzakwanilitsa zonse zimene anakuuza.”
46 Kenako Mariya anati: “Ndikulemekeza* Yehova,
47 ndipo mtima wanga ndi wokondwa kwambili cifukwa ca Mulungu, Mpulumutsi wanga,
48 cifukwa waona malo otsika a ine kapolo wake wamkazi. Ndipo kuyambila tsopano mpaka m’tsogolo, mibadwo yonse idzandichula wacimwemwe,
49 cifukwa wamphamvuyo wandicitila zazikulu ndipo dzina lake ndi loyela.
50 Ku mibadwomibadwo, iye amacitila cifundo anthu amene amamuopa.
51 Iye wacita zinthu zamphamvu ndi dzanja lake. Wabalalitsa anthu amene ndi odzikuza m’mitima yawo.
52 Watsitsa anthu amphamvu pa mipando yacifumu, ndipo wakweza anthu onyozeka.
53 Wakhutitsa anjala ndi zinthu zabwino, koma olemela wawabweza cimanjamanja.
54 Wathandiza Isiraeli mtumiki wake pokumbukila cifundo cake kwamuyaya,
55 monga anakambila kwa makolo athu akale, Abulahamu ndi mbadwa* zake.”
56 Mariya anakhala ndi Elizabeti pafupifupi miyezi itatu, kenako anabwelela kwawo.
57 Tsopano nthawi inakwana yakuti Elizabeti abeleke mwana, ndipo anabeleka mwana wamwamuna.
58 Anthu okhala naye pafupi, ndi acibale ake, anamva kuti Yehova wamuonetsa cifundo cacikulu, ndipo anakondwela naye limodzi.
59 Pa tsiku la 8, iwo anabwela kuti amucite mdulidwe mwanayo, ndipo anafuna kum’patsa dzina la atate ake lakuti Zekariya.
60 Koma mayi ake anakamba kuti: “Iyayi! dzina lake akhale Yohane.”
61 Iwo atamva izi anamuuza kuti: “Palibe wacibale wako aliyense wochedwa ndi dzina limeneli.”
62 Ndiyeno iwo anafunsa tate wake mocita kulankhula ndi manja kuti awauze dzina limene anali kufuna kum’patsa mwanayo.
63 Iye anapempha kuti am’patse polemba, ndipo analembapo kuti: “Dzina lake ndi Yohane.” Anthu onsewo ataona izi, anadabwa kwambili.
64 Nthawi yomweyo pakamwa pake panatseguka, ndipo lilime lake linamasuka moti anayamba kulankhula ndi kutamanda Mulungu.
65 Anthu onse okhala m’delalo anagwidwa ndi mantha, ndipo nkhani imeneyi inali m’kamwam’kamwa m’dela lonse la mapili la Yudeya.
66 Ndipo onse amene anamva zimenezi anayamba kuganizilapo mozama, n’kumati: “Kodi mwana ameneyu adzakhala wotani?” Cifukwa dzanja la Yehova linalidi pa iye.
67 Ndiyeno Zekariya tate wake anadzazidwa ndi mzimu woyela, ndipo ananenela kuti:
68 “Yehova Mulungu wa Isiraeli atamandike cifukwa wakumbukila anthu ake ndiponso wawabweletsela cipulumutso.
69 Watiutsila mpulumutsi wamphamvu* m’nyumba ya Davide mtumiki wake.
70 Izi n’zimene anakambilatu kupitila mwa aneneli ake oyela akale,
71 zakuti adzatipulumutsa kwa adani athu komanso m’manja mwa onse odana nafe.
72 Adzakwanilitsa zimene analonjeza makolo athu akale ndi kuwaonetsa cifundo. Ndipo adzakumbukila cipangano cake coyela,
73 lumbilo limene analumbila kwa Abulahamu kholo lathu,
74 kuti pambuyo potipulumutsa m’manja mwa adani athu, atipatse mwayi wocita utumiki wopatulika kwa iye mopanda mantha,
75 mokhulupilika, komanso mwacilungamo pamaso pake masiku athu onse.
76 Koma ponena za iwe mwana wamng’onowe, udzachedwa mneneli wa Wapamwambamwamba, cifukwa Yehova adzakutumiza patsogolo pake kuti ukakonze njila zake,
77 komanso kuti ukalengeze kwa anthu ake uthenga wa cipulumutso cimene cidzatheka Mulungu akadzawakhululukila macimo awo,
78 cifukwa ca cifundo ca Mulungu wathu. Mwa cifundo cake cimeneci, kuwala kwa m’mamawa kudzatifikila kucokela kumwamba,
79 kuti anthu okhala mu mdima ndi mu mthunzi wa imfa aone kuwala. Kuwala kumeneko kudzatsogolelanso mapazi athu pa njila ya mtendele.”
80 Conco mwana wamng’onoyo anakula, ndipo anakhala wolimba kuuzimu. Iye anapitiliza kukhala ku cipululu mpaka tsiku limene anadzionetsa poyela kwa Aisiraeli.
Mawu a m'Munsi
^ Kapena kuti, “timaziona kuti n’zodalilika.”
^ Kapena kuti, “Malinga ndi mwambo wa ansembe.”
^ Kapena kuti, “akali m’mimba mwa mayi ake.”
^ M’cinenelo coyambilila, “akatembenuze mitima ya atate kwa ana.” Izi zitanthauza kuti adzakhala ndi mtima wodzicepetsa.
^ Kapena kuti, “utumiki wotumikila anthu.”
^ Kapena kuti, “anamutomela.”
^ Kapena kuti, “Palibe ciliconse cimene Mulungu wakamba cimene cingalepheleke.”
^ Kapena kuti, “Moyo wanga ukulemekeza.”
^ M’cinenelo coyambilila, “mbewu.”
^ M’cinenelo coyambilila, “nyanga yacipulumutso.”