Mmene Mungagwiritsire Ntchito iPad, iPhone, ndi iPod touch
Onerani vidiyoyi kuti mudziwe zinthu zosiyanasiyana za pa JW Laibulale zimene zingakuthandizeni. Pezani mayankho amafunso amene anthu amakonda kufunsa okhudza pulogalamuyi.
Zatsopano
December 2024 (Version 15.1)
Zinayamba kutheka kufufuza zinthu za chinenero chamanja polemba mawu.
Panaikidwa njira zina zokuthandizani kusinthasintha liwiro la vidiyo kapena zinthu zongomvetsera.
June 2024 (Version 15.0)
Inayamba kukhala ndi zinthu za chinenero chamanja.
Masamba a Zimene Zili M’magazini kapena M’buku akumakhala ndi zithunzi zapachikuto cha bukulo likayamba kuonekera.
Mfundo zikuluzikulu za m’Baibulo komanso mabuku ena zimaonekera kumanja kwa tsambalo. Simungathe kuchita editi mfundo zikuluzikuluzi.
Nkhani yatsopano ya mu Nsanja Olonda yomwe muphunzire imaoneka mukangotsegula pa Misonkhano.
April 2024 (Version 14.3)
Mu Baibulo, gwiritsirani ntchito kachizindikiro ka mfundo zina kuti muone malifalensi ogwirizana ndi vesilo omwe akuphatikizapo malifalensi a mu Buku Lofufuzira Nkhani.
Notsi zomwe mwalemba zimaonekera pamwamba pa gawo lothandiza pophunzira.
M'CHIGAWO ICHI
Mafunso Ofunsidwa Kawirikawiri Okhudza JW Library (Pa Zipangizo za iOS)
Pezani mayankho a mafunso ofunsidwa kawirikawiri.