Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Zimene Madokotala Akunena Masiku Ano pa Nkhani Yoika Magazi Anthu Odwala

Zimene Madokotala Akunena Masiku Ano pa Nkhani Yoika Magazi Anthu Odwala

Kwa zaka zambiri, a Mboni za Yehova akhala akunyozedwa chifukwa chokana kuikidwa magazi akadwala. Iwo amakana kuikidwa magazi pomvera lamulo la m’Baibulo lakuti ‘mupewe magazi.’ A Mboni amakana kuikidwa magazi ngakhale kuti madokotala amaona kuti kuika magazi kungathandize munthu wodwala.​—Machitidwe 15:29.

Koma masiku ano madokotala ambiri odziwa bwino ntchito yawo akunena kuti pali zifukwa zabwino zogwirizana ndi nkhani zaumoyo zopewera kuika magazi anthu odwala. M’malomwake, madokotalawo akuona kuti ndi bwino kuthandiza odwala popanda kuwaika magazi.

Magazini yofotokoza nkhani za mankhwala (Stanford Medicine Magazine) yomwe inatuluka kumayambiriro kwa chaka cha 2013 ndipo imafalitsidwa ndi yunivesite ya Stanford University School of Medicine, inali ndi lipoti lapadera lokhudza nkhani ya magazi. M’lipotilo munali mutu wakuti, “Kulimbana ndi Chizolowezi Choika Magazi Anthu Odwala.” (Against the Flow​—What’s Behind the Decline in Blood Transfusions?) Amene analemba nkhaniyi ndi Mayi Sarah C. P. Williams, ndipo anati: “Kwa zaka 10 zapitazi, kafukufuku amene wakhala akuchitika wasonyeza kuti m’zipatala za padziko lonse lapansi, magazi amene anthu amapereka mwakufuna kwawo akugwiritsidwa ntchito kwambiri kuposa mmene akufunikira pothandiza odwala. Izi zikuchitika pochita opaleshoni anthu odwala komanso pothandiza odwala ena.”

Polemba nkhaniyi, Mayi Williams analemba zimene dokotala wina wotchedwa Patricia Ford ananena. Dokotalayu ndi amene anayambitsa dipatimenti yoona zothandiza odwala popanda kugwiritsa ntchito magazi (The Center for Bloodless Medicine) pachipatala chotchedwa Pennsylvania Hospital. Dr. Ford anati: “Madokotala ambiri anaphunzitsidwa zoti munthu akhoza kufa ngati magazi ake atachepa n’kufika pa muyezo winawake, komanso zoti magazi amapulumutsa moyo . . . Nthawi zina zimenezi zimakhala zoona, * koma nthawi zambiri sizikhala choncho.”

Mayi Ford, amene chaka chilichonse amathandiza odwala a Mboni za Yehova pafupifupi 700, ananenanso kuti: “Madokotala ambiri amene ndalankhulapo nawo . . . anali ndi maganizo olakwika akuti odwala ambiri sangachire ngati atapanda kuikidwa magazi . . . Nanenso ndinkakhulupirira zimenezi. Koma ndaphunzira kuti n’zotheka kuthandiza bwinobwino odwala pogwiritsa ntchito njira zina zosavuta m’malo mowaika magazi.”

Mu August 2012, magazini inanso (Archives of Internal Medicine) inafalitsa zotsatira za kafukufuku wokhudza kuchita opaleshoni anthu odwala matenda a mtima. Kafukufukuyu anachitika pachipatala chinachake kwa zaka 28. Zotsatira za kafukufukuyu zinasonyeza kuti a Mboni za Yehova ankachira msanga poyerekezera ndi odwala ena amene ankaikidwa magazi. A Mboniwo ankachira popanda mavuto ambiri, ankachira mwachangu ndiponso ankakhala ndi moyo kwa zaka zina 20 pambuyo pochitidwa opaleshoni poyerekezera ndi odwala amene ankaikidwa magazi.

Nkhani ina imene inafalitsidwa pa April 8, 2013, m’magazini ya The Wall Street Journal inanena kuti: “Kwa zaka zambiri, anthu amene amakana kuikidwa magazi chifukwa cha zimene amakhulupirira pa nkhani zokhudza chipembedzo, akhala akuchitidwa opaleshoni popanda kuwaika magazi. Masiku ano zipatala zambiri zayamba kuthandiza odwala popanda kuwaika magazi . . . Madokotala amene amalimbikitsa njira zochitira opaleshoni odwala popanda kuwaika magazi, akunena kuti njirazi n’zothandiza chifukwa sawononga ndalama zogulira magazi, zosungira magazi, kuwakonza, kuwayeza ndi kuwaika m’thupi la odwala. Kuwonjezera pamenepa, njirazi n’zothandiza kwambiri chifukwa zimachepetsa mpata woti odwala angatenge matenda ena kudzera m’magazi komanso zimachepetsa mavuto amene angachititse kuti odwala akhale nthawi yaitali m’chipatala.”

Choncho n’zosadabwitsa kuti Robert Lorenz, yemwe ndi dokotala woyang’anira nkhani zokhudza kuika magazi anthu odwala pachipatala cha Cleveland Clinic, anena kuti: “Pa nthawi imene ukuika magazi munthu wodwala, umachita kuona kuti ee, koma apa ndiye ndikuthandizadi munthuyu . . . Koma zimene zimachitikira wodwalayo zimakhala zosiyana ndi zimene umaganiza.”

^ ndime 5 Kuti mudziwe zimene a Mboni za Yehova amakhulupirira pa nkhani ya kuikidwa magazi, werengani nkhani yakuti, “N’chifukwa Chiyani Mumakana Kuikidwa Magazi?” Nkhaniyi mungaipeze pagawo lakuti “Mafunso Ofunsidwa Kawirikawiri.”