KUFOTOKOZA MAVESI A M’BAIBULO
2 Timoteyo 1:7—“Mulungu sanatipatse mzimu wamantha.”
“Pakuti Mulungu sanatipatse mzimu wamantha, koma wamphamvu, wachikondi, ndi woti tiziganiza bwino.”—2 Timoteyo 1:7, Baibulo la Dziko Latsopano.
“Pakuti Mulungu sanatipatsa mzimu wa mantha; komatu wa mphamvu ndi chikondi ndi chidziletso.”—2 Timoteo 1:7, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu.
Tanthauzo la 2 Timoteyo 1:7
Mulungu akhoza kuthandiza munthu kuti alimbe mtima n’kuchita zinthu zoyenera. Iye safuna kuti munthu aliyense akhale ndi ‘mantha’ mpaka kufika polephera kuchita zinthu zomwe Mulunguyo amasangalala nazo.
Taganizirani makhalidwe atatu ochokera kwa Mulungu otchulidwa m’vesili omwe angatithandize kuthetsa mantha.
‘Mphamvu.’ Akhristu akhala akutumikira Mulungu molimba mtima m’nthawi zovuta ngakhale pomwe akuopsezedwa ndi adani oopsa. Iwo sanabwerere m’mbuyo chifukwa cha mantha. (2 Akorinto 11:23-27) Kodi amakwanitsa bwanji kuchita zimenezi? Mtumwi Paulo anafotokoza kuti: “Pa zinthu zonse, ndimapeza mphamvu kuchokera kwa iye amene amandipatsa mphamvu.” (Afilipi 4:13) Mulungu angathe kupereka “mphamvu yoposa yachibadwa” kwa anthu omwe amamulambira ndi cholinga choti alimbane ndi vuto lililonse lomwe angakumane nalo.—2 Akorinto 4:7.
‘Chikondi.’ Kukonda kwambiri Mulungu kungathandize Mkhristu kuti alimbe mtima n’kuchita zinthu zoyenera. Komanso Mkhristu akamakonda anthu ena, zimamulimbikitsa kuti aziganizira zofuna za ena kuposa zake ngakhale atamatsutsidwa kapena kuopsezedwa.—Yohane 13:34; 15:13.
‘Kuganiza bwino.’ M’Baibulo, mawu akuti kuganiza bwino, kwenikweni amatanthauza zimene zimachitika kuti Mkhristu akwanitse kusankha zochita mogwirizana ndi mfundo za m’Baibulo. Munthu amene ndi woganiza bwino, amachitabe zinthu mwanzeru komanso mosamala ngakhale pomwe wakumana ndi mavuto. Amathabe kusankha zinthu mogwirizana ndi maganizo a Mulungu chifukwa amadziwa kuti ubwenzi wake ndi Mulungu ndi wofunika kwambiri kuposa mmene anthu ena akuonera zinthu.
Nkhani Yonse ya 2 Timoteyo 1:7
Buku la 2 Timoteyo linalembedwa ndi mtumwi Paulo ndipo inali kalata yomwe ankalembera Timoteyo yemwe anali mnzake wokondedwa komanso wantchito mnzake. M’kalatayi, mokoma mtima Paulo analimbikitsa Timoteyo amene pa nthawiyi anali wachinyamata, kuti apitirize kugwira ntchito mwakhama muutumiki. (2 Timoteyo 1:1, 2) N’kutheka kuti Timoteyo anali wamanyazi ndipo zimenezi zikanatha kumulepheretsa kuti asamachite zambiri mumpingo. (1 Timoteyo 4:12) Koma apa Paulo anakumbutsa Timoteyo kuti analandira mphatso kapena kuti utumiki wapadera mumpingo. Anamulimbikitsa kuti asamaope kugwiritsa ntchito udindo womwe anali nawo monga woyang’anira mumpingo. Anamulimbikitsanso kuti asamaope kugwiritsa ntchito udindo wake akamalalikira uthenga wabwino komanso kuti azipirira pokumana ndi mayesero kuti chikhulupiriro chake chisafooke.—2 Timoteyo 1:6-8.
Ngakhale kuti mawuwa kwenikweni analembera Timoteyo, koma amatsimikizira onse omwe akufuna kutumikira Mulungu masiku ano, kuti Yehova adzawathandiza ndi zonse zofunikira kuti zinthu ziwayendere bwino ngakhale atakumana ndi mavuto otani.