Kodi Makolo Angatani Kuti Aphunzitse Ana Awo Nkhani Zokhudza Kugonana?
Yankho la m’Baibulo
Kodi ndani amene ayenera kuphunzitsa ana nkhani zokhudza kugonana? Baibulo limapereka udindo umenewu kwa makolo, ndipo makolo ambiri aona kuti kutsatira malangizo otsatirawa n’kothandiza:
Musamachite manyazi. Baibulo limanena mosapita m’mbali nkhani zokhudza kugonana komanso ziwalo zobisika, ndipo Mulungu anauza mtundu wa Isiraeli kuti “ana” aziphunzitsidwa nkhani zoterezi. (Deuteronomo 31:12; Levitiko 15:2, 16-19) Mungagwiritse ntchito mawu olemekezeka potchula ziwalo zobisika kapena pokambirana nkhani zogonana n’cholinga choti nkhaniyo ikhale yosachititsa manyazi.
Muziwaphunzitsa pang’onopang’ono. Mwana wanu akafika paunyamata, musamuuze zonse zokhudza kugonana pa nthawi imodzi, koma muzimuuza pang’onopang’ono mogwirizana ndi msinkhu wake.—1 Akorinto 13:11.
Muziwaphunzitsa mfundo za makhalidwe abwino. N’zoona kuti ana angaphunzire zinthu zina zokhudza kugonana monga mbali ya maphunziro awo kusukulu. Komabe, Baibulo limalimbikitsa makolo kuti kuwonjezera pa kuphunzitsa ana awo nkhani zokhudza kugonana, aziwaphunzitsanso kuti adziwe anthu okhawo amene ndi oyenerera kugonana.—Miyambo 5:1-23.
Muzimvetsera. Mwana wanu akakufunsani nkhani zokhudza kugonana, musamukalipire komanso musafulumire kuganiza kuti wayamba khalidwe loipa. M’malomwake, mukhale “wofulumira kumva, wodekha polankhula.”—Yakobo 1:19.
Zimene mungachite kuti muteteze ana anu kwa anthu ogwirira
Muyambe ndinu kuphunzira. Yesetsani kudziwa zimene anthu okonda kugwirira amachita.—Miyambo 18:15; onani mutu 32 wa buku lachingelezi lakuti Questions Young People Ask—Answers That Work, Volume 1.
Muzidziwa zimene zikuchitikira mwana wanu. Musamangosiyira anthu ena mwana wanu musanatsimikizire kuti anthuwo ndi odalirika, komanso ‘musamangomulekerera’ mwana wanuyo.—Miyambo 29:15.
Mumuphunzitse kuti asamangomvera zilizonse. Ana amafunika kuphunzitsidwa kuti azimvera makolo awo. (Akolose 3:20) Komabe, ngati mungaphunzitse mwana wanu kuti azimvera chilichonse chimene munthu aliyense wamkulu angamuuze, ndiye kuti anthu ogwirira akhoza kumupezerera. Makolo omwe ndi Akhristu angauze mwana wawo kuti, “Munthu wina aliyense akakuuza kuti uchite zinthu zimene Mulungu amati n’zoipa, usachite.”—Machitidwe 5:29.
Muziyeserera zimene angachite ngati akufuna kugwiridwa. Thandizani mwana wanu kuti adziwe zimene angachite ngati munthu wina akufuna kumugwira inu kulibe. Chitani chitsanzo chokhala ngati sewero pofuna kuthandiza mwana wanuyo mmene angakanire molimba mtima kuti, “Mulekeretu zimenezo! Ndikunenerani!” kenako athawe. Mungafunike kumayeserera zimenezi “nthawi ndi nthawi” chifukwa ana sachedwa kuiwala.—Deuteronomo 6:7.